Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Akhristu Oona Amadziŵika na Cikondi—Kondwelani na Coonadi

Akhristu Oona Amadziŵika na Cikondi—Kondwelani na Coonadi

CIFUKWA CAKE N’KOFUNIKA: Potengela citsanzo ca Yesu, tifunika kucitila umboni coonadi cokamba za colinga ca Mulungu. (Yoh. 18:37) Tifunikanso kukondwela na coonadi, kumakamba zoona komanso kumaganizila zilizonse za zoona, olo kuti tikukhala m’dziko lodzala mabodza ndiponso limene limacita zosalungama.—1 Akor. 13:6; Afil. 4:8.

MMENE TINGACITILE:

  • Tsimikizani mtima kuti musamamvele kapena kufalitsa misece.—1 Ates. 4:11

  • Musamakondwele wina akamavutika

  • Muzikondwela na zinthu zabwino ndiponso zolimbikitsa

TAMBITSANI VIDIYO YAKUTI “MUZIKONDANA”—KONDWELANI NDI COONADI OSATI NDI ZOSALUNGAMA, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi mlongo Debbie “anakondwela ndi zosalungama” m’lingalilo lanji?

  • Nanga mlongo Alice anasintha bwanji makambilano awo na mlongo Debbie kuti akhale oyenela?

  • Ni zinthu zabwino ziti zimene tingakambilane?

Kondwelani na coonadi osati na zosalungama