Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 18-19

Yesu Anacitila Umboni Coonadi

Yesu Anacitila Umboni Coonadi

18:36-38a

Yesu anacitila umboni coonadi cokhudza colinga ca Mulungu

  • M’MAWU: Mokangalika iye anali kulalikila coonadi conena za Ufumu wa Mulungu

  • M’ZOCITA: Umoyo wake unaonetsa poyela kuti maulosi a Mulungu amakwanilitsika

Pokhala ophunzila a Yesu, na ise timacitila umboni coonadi

  • M’MAWU: Ngakhale ena atinyoze, mokangalika timalalikila uthenga wabwino wonena za kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu, umene Khristu ndiye Mfumu yake

  • M’ZOCITA: Timaonetsa kuti tikucilikiza ufumu wa Yesu mwa kuyesetsa kukhala na makhalidwe aumulungu komanso mwa kupewa kutengako mbali m’zandale