October 12-18
EKSODO 33-34
Nyimbo 115 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Makhalidwe Abwino a Yehova”: (10 min.)
Eks. 34:5—Kudziŵa dzina la Mulungu kumatanthauza kudziŵa zolinga zake, zocita zake, na makhalidwe ake (it-2 466-467)
Eks. 34:6—Makhalidwe a Yehova amatisonkhezela kumuyandikila (w09 5/1 18 ¶3-5)
Eks. 34:7—Yehova amakhululukila anthu ocimwa amene alapa (w09 5/1 18 ¶6)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Eks. 33:11, 20—Kodi Yehova analankhula motani na Mose “pamasom’pamaso”? (w04 3/15 27 ¶5)
Eks. 34:23, 24—N’cifukwa ciani amuna aciisiraeli anali kufunika kukhala na cikhulupililo kuti akapezeke pa zikondwelelo zitatu za pacaka? (w98 9/1 20 ¶5)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Eks. 33:1-16 (th phunzilo 10)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako: (5 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi, ndiyeno funsani mafunso otsatilawa: Kodi Brandi wafotokoza bwanji momveka bwino mmene tingaseŵenzetsele mfundo ya pa lemba? Nanga wacita ciani pothandiza mwininyumba kuganiza?
Ulendo Wobwelelako: (3 min. olo kucepelapo) Mukayamba makambilano acitsanzo, mwininyumba akambe mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki. Koma mwaluso, loŵelani pa mawu amenewo. (th phunzilo 16)
Ulendo Wobwelelako: (5 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Kenako gaŵilani buku lakuti Zimene Baibulo Ingatiphunzitse na kuyambitsa phunzilo pa nkhani 2. (th phunzilo 8)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Acinyamata—Kodi Yehova ni Bwenzi Lanu Lapamtima?”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Acinyamata—“Talawani ndipo muone kuti Yehova ndi wabwino”.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min. olo kucepelapo) jy mutu 136
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 103 na Pemphelo