October 19-25
EKSODO 35-36
Nyimbo 92 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Anapatsidwa Nzelu Kuti Agwile Nchito ya Yehova”: (10 min.)
Eks. 35:25, 26—Yehova anadalitsa anthu ake cifukwa ca mtima wawo wodzipeleka (w14 12/15 4 ¶4)
Eks. 35:30-35—Mzimu woyela unathandiza Bezaleli na Oholiabu kukhala na luso logwila “nchito ina iliyonse” (w11 12/15 19 ¶6)
Eks. 36:1, 2—Yehova ndiye analandila citamando cifukwa ca nchito imene iwo anagwila (w11 12/15 19 ¶7)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Eks. 35:1-3—Kodi tiphunzilapo ciani pa lamulo la Sabata? (w05 5/15 23 ¶14)
Eks. 35:21—N’cifukwa ciani mzimu wodzipeleka wa Aisiraeli ni citsanzo cabwino kwa ife? (w00 11/1 29 ¶1)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Eks. 35:1-24 (th phunzilo 11)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (3 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 11)
Ulendo Wobwelelako: (4 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno uzani mwininyumba za webusaiti yathu, na kumugaŵila kakhadi kongenela pa webusaiti. (th phunzilo 4)
Phunzilo la Baibo: (5 min. olo kucepelapo) bhs 26 ¶18-20 (th phunzilo 19)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Lipoti ya 2018 ya Komiti Yoyang’anila Nchito Yofalitsa: (15 min.) Tambitsani vidiyoyi. Ndiyeno funsani omvetsela mafunso aya: Kodi gulu lathu lapanga masinthidwe otani pa nchito yopulinta mabuku, nanga n’cifukwa ciani? Ni zinthu ziti zimene zapita patsogolo cifukwa ca kucepa kwa nchito yopulinta mabuku? Kodi nchito yomasulila yathandiza bwanji pokonza cakudya cauzimu? Kodi nchito yopanga zofalitsa za pa intaneti komanso mavidiyo yakhala na zotulukapo zabwino ziti?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min. olo kucepelapo) jy mutu 137
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 69 na Pemphelo