UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kampeni Yapadela Yolengeza za Ufumu wa Mulungu mu November
Yesu anali kulengeza “uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.” (Luka 4:43) Komanso anaphunzitsa anthu kuti azipemphelela Ufumuwo kuti ubwele. (Mat. 6:9, 10) M’mwezi wa November, tidzakhala na nchito yapadela yolengeza mwakhama za Ufumu wa Mulungu. (Mat. 24:14) Konzani zinthu pa umoyo wanu kuti mukatengeko mbali mokwanila pa kampeni imeneyo. Onse amene adzacita upainiya wothandiza m’mwezi umenewu, adzakhala na ufulu wosankha kulalikila maola 30 kapena 50.
Pocita kampeniyo, mukaŵelenge lemba lokamba za Ufumu wa Mulungu kwa anthu ambili a m’gawo lanu mmene mungathele. Posankha lemba loŵelenga, ganizilani zikhulupililo za anthu a m’gawo lanu. Ngati winawake waonetsa cidwi pa ulendo woyamba, m’gaŵileni Nsanja ya Mlonda yogaŵila ya Na. 2 2020. Mukatelo, mukabweleleko mwamsanga, ndipo mudzayesetse kuyambitsa phunzilo la Baibo poseŵenzetsa cimodzi mwa zida za mu Thuboksi yathu. Nthawi yangotsala pang’ono kuti Ufumu wa Mulungu uphwanye maboma onse otsutsana nawo. (Dan. 2:44; 1 Akor. 15:24, 25) Conco, tiyeni tiuseŵenzetse mokwanila mwayi wapadela umenewu, poonetsa kuti ndife okhulupilika kwa Yehova na Ufumu wake!