October 5-11
EKSODO 31-32
Nyimbo 45 na Pemphelo
Mawu Oyamba (1 min.)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Pewani Kupembedza Mafano”: (10 min.)
Eks. 32:1—Kukumana na mavuto si cifukwa cakuti munthu ayambe kutumikila milungu ina (w09 5/15 11 ¶11)
Eks. 32:4-6—Aisiraeli anasakaniza kulambila koona na kulambila konama (w12 10/15 25 ¶12)
Eks. 32:9, 10—Mkwiyo wa Yehova unawayakila Aisiraeli (w18.07 20 ¶14)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (10 min.)
Eks. 31:17—Kodi Yehova anapuma pa tsiku la 7 la kulenga m’lingalilo lotani? (w19.12 3 ¶4)
Eks. 32:32, 33—Tidziŵa bwanji kuti ciphunzitso cakuti “munthu akangolandila Khristu ndiye kuti basi wapulumutsidwa” n’cabodza? (w87 9/1 29)
Pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Eks. 32:15-35 (th phunzilo 10)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi, ndiyeno funsani mafunso aya: Kodi Brandi waseŵenzetsa bwanji mafunso mwaluso? Kodi wayala bwanji maziko a ulendo wobwelelako?
Ulendo Woyamba: (4 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno chulani na kukambilana vidiyo yakuti N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo? (koma musaitambitse) (th phunzilo 9)
Nkhani: (5 min. olo kucepelapo) w10 5/15 21—Mutu: N’cifukwa Ciani Yehova Sanam’lange Aroni Atapanga Fano la Mwana wa Ng’ombe? (th phunzilo 7)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Muziona Ubale Wanu na Yehova Kukhala Wamtengo Wapatali”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Tetezani Ubale Wanu na Yehova (Akol. 3:5).
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min. olo kucepelapo) jy mutu 135
Mawu Othela (3 min. olo kucepelapo)
Nyimbo 90 na Pemphelo