UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Muziona Ubale Wanu na Yehova Kukhala Wamtengo Wapatali
Ife Mboni za Yehova tili na mwayi wapadela. Pokhala Akhristu odzipatulila komanso obatizika, timapitiliza kupanga ubale wolimba na Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Anatikokela kwa iye kupitila mwa Mwana wake. (Yoh. 6:44) Iye amamvetsela mapemphelo athu.—Sal. 34:15.
Kodi tingateteze bwanji ubale wathu wamtengo wapatali na Mulungu? Cimodzi cimene tiyenela kucita ni kupewa macimo ngati amene Aisiraeli anacita. Iwo atangocita pangano na Yehova, anapanga mwana wang’ombe wagolide n’kuyamba kumulambila. (Eks. 32:7, 8; 1 Akor. 10:7, 11, 14) Tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi nimacita bwanji nikakumana na mayeselo? Kodi zocita zanga zimaonetsa kuti nimaona ubale wanga na Yehova kukhala wamtengo wapatali?’ Kukonda kwambili Atate wathu wakumwamba kudzatithandiza kupewa kucita zinthu zimene iye amazonda. —Sal. 97:10.
TAMBANI VIDIYO YAKUTI TETEZANI UBALE WANU NA YEHOVA (AKOL. 3:5), NDIPO PAMBUYO PAKE YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
-
Kodi kusilila kwa nsanje n’ciani?
-
N’cifukwa ciani tiyenela kupewa dyela na kulambila mafano?
-
Kodi cigololo na kulambila mafano n’zogwilizana bwanji?
-
N’cifukwa ciani maka-maka abale amene ali pa udindo afunika kuyesetsa kusamalila zosoŵa za mnzawo wa m’cikwati?