Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHIRISTU

Mukapeza Mwana Panyumba

Mukapeza Mwana Panyumba

Tikapeza mwana panyumba, tingamuuze kuti tifuna kukambako ndi makolo ake. Kucita zimenezi kumaonetsa kuti tikulemekeza makolo ake amene ali ndi udindo womulangiza. (Miy. 6:20) Mwana akatiuza kuti tiloŵe m’nyumba, tisathamangile kulowa. Ngati makolo palibe, tingapeze nthawi ina yopitakonso.

Ngakhale mwanayo atakhala wamkulu, mwina wa zaka zapakati pa 15 ndi 19, tingacite bwino kumupempha kuti tikambe na makolo ake. Ngati makolowo palibe, tingamufunse ngati amamuvomeleza kudzisankhila zinthu zoŵelenga. Ngati amamuvomeleza, tingamugaŵile cofalitsa kapena kumuuza za webusaiti yathu ya jw.org.

Pocita ulendo wobwelelako kwa wacicepele amene waonetsa cidwi, tingamuuze kuti tifuna kuonana ndi makolo ake. Kucita zimenezi kudzatipatsa mwayi wofotokozela makolowo colinga ca ulendo wathu, ndiponso tidzatha kuwafotokozela malangizo odalilika opezeka m’Baibulo okhudza banja. (Sal. 119:86, 138) Kucitila ulemu makolo ndi kuwaganizila kudzatithandiza kukhala alaliki abwino, ndipo kudzatipatsanso mpata wina wolalikila ena m’banjalo.—1Pet 2:12.