Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MASALIMO 135-141

Tinapangidwa Modabwitsa

Tinapangidwa Modabwitsa

Davide anali kuganizila za umboni woonetsa makhalidwe abwino a Mulungu amene amaonekela m’zinthu zimene anapanga. Iye anaseŵenzetsa moyo wake kutumikila Yehova mokhulupilika.

Davide ataganizila kwambili za cilengedwe, anayamba kutamanda Yehova:

139:14

  • “Ndidzakutamandani cifukwa munandipanga modabwitsa”

139:15

  • “Mafupa anga sanali obisika kwa inu pamene munali kundipanga m’malo obisika, pamene munali kundiwomba ngati nsalu m’malo apansi kwambili padziko lapansi”

139:16

  • “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu”