Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHIRISTU

Zimene Tiyenela Kupewa Pocititsa Phunzilo la Baibulo

Zimene Tiyenela Kupewa Pocititsa Phunzilo la Baibulo

Kukamba Kwambili: Musaganize kuti mufunika kufotokoza zonse. Yesu anaseŵenzetsa mafunso kuti athandize anthu kuganiza ndi kuona zimene afunika kucita. (Mat. 17:24-27) Mafunso amacititsa phunzilo kukhala logwila mtima. Angakuthandizeni kudziŵa ngati wophunzila akumvetsetsa zimene akuphunzila ndi kuzikhulupilila. (be-CN, tsa. 253 ndime 3-4) Mukafunsa funso, muzileza mtima n’kuyembekezela yankho. Ngati wophunzila wapeleka yankho lolakwika, musamuyankhile. M’malomwake, m’thandizeni kupeza yankho mwa kumufunsa mafunso ena owonjezela. (be tsa. 238 ndime 1-2) Musafotokoze mothamanga mfundo zatsopano kuti wophunzila amvetsetse.—be-CN, tsa. 230 ndime 4.

Kufotokoza Zambili: Pewani kukamba zonse zimene mudziŵa pa nkhani imene muphunzila. (Yoh. 16:12) Kambani cabe mfundo yaikulu m’ndime. (be-CN, tsa. 226 ndime 4-5) Zinthu zina, ngakhale n’zocititsa cidwi zingangophimba mfundo yaikulu. (be-CN, tsa. 235 ndime 3) Ngati wophunzila wamvetsetsa mfundo yaikulu, pitani m’ndime yotsatila.

Kufuna Kutsiliza Buku: Colinga cathu si kutsiliza buku, koma kufika pamtima pa wophunzila. (Luka 24:32) Lolani mphamvu ya Mau a Mulungu kugwila nchito mwa munthuyo mwa kufotokoza malemba a mfundo zazikulu za m’nkhaniyo. (2 Akor. 10:4; Aheb. 4:12; be-CN, tsa. 144 ndime 1-3) Seŵenzetsani mafanizo osavuta kumva. (be-CN, tsa. 245 ndime 2-4) Dziŵani mavuto ndi zikhulupililo za wophunzila, ndipo fotokozani mfundo zogwilizana ndi umoyo wake. M’funseni mafunso monga akuti: “Mumvela bwanji ndi zimene muphunzila?” “Kodi zimenezi zitiphunzitsa ciani za Yehova?” “Muona kuti mungapindule bwanji ngati museŵenzetsa mfundo izi?”—be-CN, tsa. 238 ndime 3-5; tsa. 259 ndime 1.