Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyambitsa Makambilano Otsogolela ku Ulaliki

Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuyambitsa Makambilano Otsogolela ku Ulaliki

Poyamba na kuceza cabe na mzimayi wacisamariya, Yesu anakwanitsa kucita ulaliki wamwayi. Kodi tinganole bwanji luso lathu loyambitsa makambilano na ŵanthu amene sitiwadziŵa?

  • Muzikamba na ŵanthu mwaubwenzi. Ngakhale kuti anali atalema, Yesu anayamba kukambilana na mayiyo mwa kungom’pempha madzi akumwa. Conco, mungayambe na moni waubwenzi, kenako n’kukambako za mmene kwacela tsikulo, kapena nkhani ina yake yodziŵika. Kumbukilani kuti, colinga coyamba ni kuyambitsa cabe makambilano. Mungakambe nkhani iliyonse imene munthu angacite nayo cidwi. Ngati sakuyankha, musadandaule. Yesaninso munthu wina. Pemphani Yehova kuti akulimbitseni mtima.—Neh. 2:4; Mac. 4:29.

  • Muziona bwino mpata woloŵetselapo ulaliki, koma osafulumila kwambili. Coyamba cezankoni cabe. Cifukwa ngati mulimbikila zakuti mulalikile, munthuyo adzamangika ndipo angaleke kulankhula. Ngati makambilano atha musanapeze mpata womulalikila, osakhumudwa. Ndipo ngati mumacita mantha kucita ulaliki wamwayi, yesani kumayambitsa makambilano popanda colinga colalikila. [Tambitsani na kukambilana vidiyo yoyamba.]

  • Yesani kupeza poloŵela kuti muyambe kulalikila mwa kukamba zimene mumakhulupilila. Zimenezi zingapangitse munthuyo kukufunsani kuti amve zambili. Yesu anakamba mawu okopa cidwi amene anapangitsa mayi uja kufunsa mafunso. Pamene anayamba kumufotokozela uthenga wabwino, Yesu anali kuyankha mafunso a mayiyo. [Tambitsani na kukambilana vidiyo yaciŵili. Pambuyo pake, tambitsani na kukambilana vidiyo yacitatu.]