September 17-23
YOHANE 5-6
Nyimbo 2 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Tsatilani Yesu na Colinga Cabwino”: (10 min.)
Yoh. 6:9-11—Yesu mozizwitsa anadyetsa khamu la anthu (“amuna pafupi-fupi 5,000 anakhaladi pansi” nwtsty mfundo younikila pa Yoh. 6:10)
Yoh. 6:14, 24—Anthu atazindikila kuti Yesu anali Mesiya, tsiku lotsatila anayamba kumufuna-funa (“mneneli uja” mfundo younikila pa Yoh. 6:14)
Yoh. 6:25-27, 54, 60, 66-69—Popeza kuti anthuwo anali kutsatila Yesu na ophunzila ake pa zolinga zadyela, anakhumudwa na mawu ake (“cakudya cimene cimawonongeka. . . cakudya cokhalitsa, copeleka moyo wosatha”, “Wakudya mnofu wanga ndi kumwa magazi anga” nwtsty mfundo zounikila pa Yoh. 6:27, 54; w05 9/1 peji 21 mapa. 13-14)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Yoh. 6:44—Kodi Atate amawakokela bwanji anthu kwa iyemwini? (“kukokedwa” nwtsty mfundo younikila)
Yoh. 6:64—Yesu anadziŵa “kucokela pa ciyambi” kutiYudasi ndiye adzamupeleka. Kodi n’kucokela pa ciyambi pati? (“Yesu anadziŵa . . . amene adzamupeleka,” “kucokela pa ciyambi” nwtsty mfundo zounikila)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Yoh. 6:41-59
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Mwininyumba akambe zimene anthu a m’gawo lanu amakonda kukamba pofuna kupewa kuwalalikila.
Kubwelelako Koyamba: (3 min. olo kucepelapo) Yambani na makambilano acitsanzo. Mwininyumba akukuuzani kuti ni Mkhristu.
Vidiyo ya Kubwelelako Kaciŵili: (5 min.) Tambitsani na kukambilana vidiyoyi.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Zinayenda Bwanji?: (5 min.) Kukambilana. Pemphani omvela kuti afotokoze mmene zinayendela atayesa kuyambitsa makambilano otsogolela ku ulaliki.
“Sipanawonongeke Ciliconse”: (10 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Kamangidwe Kosawononga Cilengedwe Kamalemekezetsa Yehova—Kambali Kake.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu. 35 mapa. 28-36
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 89 na Pemphelo