YOHANE 5-6
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU |Tsatilani Yesu na Colinga Cabwino
6:9-11, 25-27, 54, 66-69
Yesu atapeleka fanizo limene ophunzila ake analephela kulimvetsetsa, ena anakhumudwa ndipo analeka kumutsatila. Apo n’kuti Yesu atawapatsa cakudya anthuwo mozizwitsa, poonetsa kuti mphamvu zake zinali zocokela kwa Mulungu. Kodi iwo anakhumudwa cifukwa ciani? Cifukwa cakuti anali kutsatila Yesu na zolinga zadyela. Anali kungofunako zabwino zakuthupi.
Na ise tiyenela kudzifunsa kuti: Kodi nimatsatila Yesu pa colinga canji? Kodi cacikulu ni maubwino amene nimapezapo pali pano, na madalitso amene nidzalandila m’tsogolo? Kapena n’cifukwa cakuti nimakonda Yehova, na kucita zinthu zom’kondweletsa?
N’cifukwa ciani tingadzigwilitse mwala ngati zolinga zathu zazikulu potumikilaYehova ni izi?
-
Kukonda kukhala pamodzi na anthu a Mulungu
-
Kufuna kudzakhala m’Paradaiso