Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI

Landilani Thandizo la Anchito Anzanu

Landilani Thandizo la Anchito Anzanu

Pofuna kutithandiza, Yehova watipatsa “gulu lonse” la abale na alongo. (1 Pet. 5:9) Iwo angatithandize kugonjetsa zopinga zimene tingakumane nazo mu ulaliki. Mwacitsanzo, mtumwi Paulo anapindula na thandizo la Akula na Purisikila, Sila, Timoteyo, komanso ena.—Mac. 18:1-5.

Kodi anchito anzanu angakuthandizeni bwanji mu ulaliki? Angakuthandizeni kudziŵa mmene mungayankhile anthu okana kuwalalikila. Angakuthandizeninso kupanga maulendo obwelelako, komanso kuyambitsa maphunzilo a Baibo na kuwatsogoza. Ganizilani wofalitsa mumpingo amene angakuthandizeni pa mbali imene mufunika thandizo. Ndiyeno, m’pempheni kuti akuthandizeni. Mosakayikila, nonse mudzapindula, ndipo mudzapeza cimwemwe.—Afil. 1:25.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI PEZANI CIMWEMWE PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA—LANDILANI THANDIZO LA YEHOVA—ABALE ATHU, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi mlongo Neeta anam’limbikitsa bwanji Rose kuti azipezeka ku misonkhano?

  • N’cifukwa ciani tiyenela kumatengako ofalitsa ena pokatsogoza phunzilo la Baibo?

  • Ni udindo wa mpingo wonse kuthandiza munthu kuti akhale wophunzila

    Kodi Rose na mlongo Abigay anali kukonda zinthu ziti zofanana?

  • Ni maluso ati a mu ulaliki amene mungaphunzile kwa anchito anzanu?