UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Muzim’kumbukila Yehova Nthawi Zonse
Ngati zikutivuta kupeza nchito yakuthupi, cingakhale covuta kupitiliza kuika Ufumu wa Mulungu patsogolo mu umoyo wathu na cilungamo cake. Tingakhale pa mayeselo ovomela kugwila nchito imene ingasokoneze utumiki wathu kwa Yehova, kapena imene imasemphana na mfundo za m’Baibo. Komabe, tiyenela kukhala otsimikiza kuti Yehova amaonetsa mphamvu zake “kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Kulibe cimene cingalepheletse Atate wathu wacikondi kutithandiza na kutipatsa zimene timafunikila. (Aroma 8:32) Conco, pamene tipanga zisankho zokhudza nchito, tiyenela kudalila Yehova na kusumika maganizo athu pa kum’tumikila.—Sal. 16:8.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI TUMIKILANI YEHOVA NA MOYO WANU WONSE, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:
-
N’cifukwa ciani m’bale Jason anakana kulandila ciphuphu?
-
Kodi Akolose 3:23 tingaiseŵenzetse bwanji?
-
Kodi citsanzo cabwino ca m’bale Jason cinam’khudza bwanji Thomas?
-
Kodi Mateyu 6:22 tingaiseŵenzetse bwanji?