UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Pitilizani Kuphunzitsa Mphamvu Zanu za Kuzindikila
Munthu wocita maseŵela amafunika kupitiliza kucita zinthu zolimbitsa thupi lake kuti akhalebe waluso. Nafenso, tiyenela kupitiliza kuphunzitsa mphamvu zathu za kuzindikila. (Aheb. 5:14) Mwina tili na cizoloŵezi cotengela zisankho za ena. Koma tiyenela kukulitsa luntha lathu la kuganiza na kudzipangila tokha zisankho. Cifukwa ciani? Cifukwa aliyense wa ife adzadziyankhila yekha pa zisankho zimene amapanga.—Aroma 14:12.
Tisaganize kuti tizipanga zisankho zabwino, cabe cifukwa cakuti takhala m’coonadi zaka zambili. Kuti tipange zisankho zabwino, tiyenela kudalila Yehova na mtima wonse, Mawu ake, na gulu lake.—Yos. 1:7, 8; Miy. 3:5, 6; Mat. 24:45.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI “KHALANI NDI CIKUMBUMTIMA CABWINO,” KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:
-
Kodi mlongo Emma anafunika kupanga cisankho cotani?
-
N’cifukwa ciani tiyenela kupewa kukambapo maganizo athu pa nkhani zodalila cikumbumtima?
-
Ni malangizo anzelu ati amene banja lina linapatsa mlongo Emma?
-
N’kuti kumene mlongo Emma anapeza mfundo zothandiza pa vuto lake?