September 6-12
DEUTERONOMO 33-34
Nyimbo 150 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Funani Citetezo M’manja a Yehova ‘Amene Adzakhalapo Mpaka Kale-kale’”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
Deut 34:6—Kodi mwina n’cifukwa ciani Yehova sanaulule kumene anaika mtembo wa Mose? (it-2 439 ¶3)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) Deut. 33:1-17 (th phunzilo 10)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (Mph. 5) Kukambilana. Onetsani vidiyo yakuti Ulendo Woyamba: Baibo—2 Tim. 3:16, 17. Nthawi iliyonse vidiyo ikaima, na imwe iimitseni na kufunsa omvetsela mafunso amene aonekela mu vidiyo.
Ulendo Woyamba: (Mph. 3) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo. (th phunzilo 1)
Ulendo Woyamba: (Mph. 5) Yambani na makambilano acitsanzo. Ndiyeno gaŵilani bulosha yakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! na kuyambitsa phunzilo la Baibo. (th phunzilo 3)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Seŵenzetsani Buku Lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! mu Ulaliki”: (Mph. 15) Kukambilana. Onetsani vidiyo yakuti Takulandilani ku Phunzilo Lanu la Baibo. Ngati nthawi ilipo, fotokozankoni mbali zina za buku latsopano limeneli. Limbikitsani onse kuti akaŵelenge phunzilo lililonse m’buku latsopano limeneli paokha kapena pa Kulambila Kwawo kwa Pabanja.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lfb, phunzilo 54
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 115 na Pemphelo