October 10-16
1 MAFUMU 19-20
Nyimbo 33 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Muziyang’ana kwa Yehova Kuti Mupeze Citonthozo”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
1 Maf. 19:19-21—Kodi tiphunzilapo ciyani pa nkhaniyi za kulandila utumiki watsopano? (w97 11/1 31 ¶2)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulila iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) 1 Maf. 19:1-14 (th phunzilo 12)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako: (Mph. 5) Kukambilana. Onetsani vidiyo yakuti Ulendo Wobwelelako: Baibo—Yobu 26:7. Nthawi zonse vidiyo ikaima, inunso iimitseni na kufunsa omvela mafunso amene aonekela.
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 3) Makambilano anu atsamile pa mfundo yaikulu ya makambilano acitsanzo. (th phunzilo 18)
Phunzilo la Baibo: (Mph. 5) lff phunzilo 07 mfundo 7, na mbali yakuti Anthu Ena Amakamba Kuti (th phunzilo 7)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Musalefuke: (Mph. 15) Kukambilana. Onetsani vidiyoyi. Kenako funsani omvela mafunso awa: Ni mfundo za m’Baibo ziti zimene zingatithandize kuti tisalefuke tikakumana na mavuto? Kodi Yehova anam’limbikitsa bwanji Eliya? Nanga Yehova amatitonthoza bwanji na kutisamalila?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lff phunzilo 22
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 57 na Pemphelo