Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Mbali Zothandiza m’Buku Lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!

Mbali Zothandiza m’Buku Lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!

Kodi mumakondwela kuseŵenzetsa mavidiyo na mafunso amene ali m’buku lakuti, Kondwelani na Moyo Kwamuyaya? Nanga bwanji mbali zakuti “Anthu Ena Amakamba Kuti,” “Colinga,” komanso yakuti “Fufuzani”? Ni mbali zina ziti za m’bukuli zingakuthandizeni popanga ophunzila?—Mat. 28:19, 20.

Midiya: Ngati museŵenzetsa buku lopulinta potsogoza phunzilo, mungapeze bwanji mavidiyo na malifalensi onse pamalo amodzi? Mukatsegula buku la pacipangizo, sankhani cigawo cimodzi mwa zigawo zake zinayi zikulu-zikulu. Pansi pa mndandanda wa maphunzilo a m’cigawoco, pali mbali yakuti midiya ya cigawo, pamene mungapezepo mavidiyo na malifalensi onse a m’cigawoco. (Onani cithunzi 1.)

Maonekedwe a buku lopulinta: Ngati mutsogoza phunzilo m’buku la pacipangizo, zingakhale zothandiza nthawi zina kugwilitsa nchito maonekedwe a buku lopulinta. Mungacite bwanji zimenezi? Phunzilo limene mukuphunzila lili citsegukile, dinizani pa tumadoti tutatu pamwamba pa tsambalo, na kusankha pakuti “Printed Edition.” Kugwilitsa nchito maonekedwe a buku lopulinta pophunzila, kungakuthandizeni kugwilizanitsa mfundo imene mukuphunzila na mfundo yaikulu ya phunzilo lonse. Kuti mubwelele, pitaninso pa tumadoti tutatu na kusankha pa “Digital Edition.”

Mabokosi akuti “Kodi Ndine Wokonzeka?”: Mabokosiwa ali cakumapeto kwa bukuli, ndipo amafotokoza ziyenelezo zofunikila kuti munthu azilalikila na mpingo, kapena kuti abatizike. (Onani cithunzi 2.)

Mfundo za Kumapeto: Mfundozi zimafotokoza nkhani zina zofunika. M’buku la pacipangizo, kothela kwa mfundo iliyonse ya kumapeto, kuli linki imene ingakubwezeni ku phunzilo limene munali kuphunzila. (Onani cithunzi 2.)

Ngati wophunzila Baibo wabatizika musanatsilize kuphunzila buku lakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!, muyenela kupitiliza kuphunzila naye bukuli mpaka kulitsiliza. Mungapitilize kulemba maola, maulendo obwelelako, na phunzilo olo kuti wophunzilayo anabatizika kale. Ngati muli na wofalitsa wina potsogoza phunzilolo ndipo watengako mbali, nayenso angalembe maola