UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Ukwati Ni Mgwilizano wa Moyo Wonse
Banja lacikhristu likamayenda bwino, Yehova amalemekezeka komanso aŵili okwatilanawo amakhala acimwemwe. (Maliko 10:9) Kuti Akhristu akakhale na banja lolimba komanso lacimwemwe, amafunika kutsatila mosamala mfundo za m’Baibo posankha woloŵa naye m’banja.
Muyenela kuyamba cibwenzi kokha ngati mwapitilila “pacimake pa unyamata,” cifukwa pa nthawiyi cilakolako ca kugonana cimakhala camphamvu kwambili ndipo cingakulepheletseni kusankha mwanzelu. (1 Akor. 7:36) Gwilitsani nchito mwanzelu nthawi ya umbeta polimbitsa ubale wanu na Mulungu, komanso kukulitsa makhalidwe acikhristu. Mukatelo, ndiye kuti mukakaloŵa m’banja, mudzathandiza kwambili kuti banjalo likakhala lolimba.
Musanagwilizane zokwatilana na munthu winawake, muyenela kukhala na nthawi yokwanila yodziŵa umunthu wake “wobisika wa mumtima.” (1 Pet. 3:4) Ngati pali zinthu zina zodetsa nkhawa zimene mwaona, kambilanani naye munthuyo. Monga zimakhalila na maunansi ena pakati pa anthu, ngati mwaloŵa m’banja, mumafunika kuika maganizo pa zimene mungacitile mnzanuyo, osati pa zimene mufuna kuti iye akucitileni. (Afil. 2:3, 4) Mukamatsatila mfundo za m’Baibo musanaloŵe m’banja, ndiye kuti mukuyala maziko olimba a banja lacimwemwe.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI KUKONZEKELA KULOŴA M’BANJA—MBALI 3: KUWELENGELA MTENGO WAKE, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:
-
Kodi cibwenzi ca mlongoyu na Shane cinali kuyenda bwanji?
-
N’ciyani cimene mlongoyu anaona m’kupita kwa nthawi?
-
Kodi makolo ake anamuthandiza bwanji? Nanga iye anapanga cisankho cotani canzelu?