UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Pezani Nzelu Zothandiza pa Umoyo pa JW.ORG
Mawu a Mulungu amatikonzekeletsa mokwanila kupilila mavuto amene timakumana nawo masiku ano otsiliza. (2 Tim. 3:1, 16, 17) Ngakhale n’conco, nthawi zina timafunika thandizo kuti tipeze mfundo za m’Baibo zimene zingatithandize pa mbali inayake. Mwacitsanzo, kodi ndinu kholo ndipo mufuna malangizo amene angakuthandizeni kulela bwino ana? Kodi ndinu wacinyamata amene mukukumana na mavuto oyesa cikhulupililo canu? Kapena kodi mukuvutika na cisoni cifukwa munatayikilidwa mwamuna kapena mkazi wanu? Mungapeze nkhani pa jw.org zimene zingakuunikileni mfundo za m’Baibo zothandiza pa mavuto amenewa na ena ambili.—Miy. 2:3-6.
Patsamba loyambila la jw.org ku Chichewa, pitani pa ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA. (Onani cithunzi 1.) Pa mndandanda umene uli pamenepo, sankhani zimene mufuna. Kapena pitani pa LAIBULALE, kenako pa NKHANI ZOSIYANASIYANA, na kusankha zimene mufuna. (Onani cithunzi 2.) Nkhanizi zimapezekanso pa JW Laibulale®. a Mungafufuze zimene mufuna pa malo amene tachulawa. Komanso ngati mungafune, mungafufuze mwacindunji nkhani imene mufuna pogwilitsa nchito danga lofufuzila pa jw.org.
Fufuzani mfundo zili m’munsimu pa jw.org poseŵenzetsa danga lofufuzila. Ndiyeno lembani nkhani zimene mwapeza, zimene mufuna kukaŵelenga.
-
Kulela ana
-
Kupsinjika maganizo kwa acinyamata
-
Imfa ya mnzanu wa mu ukwati
a Dziŵani kuti nkhani zina palipano zimapezeka cabe pa jw.org.