UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Seŵenzetsani Tsamba Loyamba la JW.ORG mu Ulaliki
Pa tsamba loyamba la webusaiti yathu pamapezeka nkhani na mavidiyo amene anakonzedwa kuti azikopa cidwi ca anthu oona mtima amene si Mboni. (Mac. 13:48) Nthawi zambili pa tsambali pamakhala nkhani zimene zafalitsidwa pa nyuzi kapena zimene zili m’kamwa-m’kamwa.
Kodi mungaliseŵenzetse bwanji tsamba loyamba la webusaiti yathu mu ulaliki?
-
Muzionapo kaŵili-kaŵili pa webusaiti yathu. Onani nkhani zimene zili pansi pa kamutu kakuti “Zimene Zilipo” na kuganizila mmene mungaziseŵenzetsele polalikila munthu wacidwi. (Kuti mupeze nkhani zina zimene zinali pa tsamba loyamba caposacedwa, dinizani pa “Onani Zina.”) Mukamaonapo kaŵili-kaŵili pa webusaiti yathu mudzapeza mfundo zatsopano zoseŵenzetsa mu ulaliki.
-
Gwilitsani nchito nkhani na mavidiyo opezeka pa tsamba loyamba poyambitsa makambilano. Mavidiyo na nkhani zimenezi zidzakuthandizani kudziŵa zimene anthu a m’dela lanu akuganizila.
-
Onetsani anthu tsamba loyamba la webusaiti yathu. Pokambilana na munthu, muunikilen’koni nkhani zina pa tsambalo komanso muonetseni mmene angapezele zinthu pa webusaiti yathu.
-
Tumizani linki. Anthu ena safuna kukamba nafe pamaso-m’pamaso koma amavomela kupita pa webusaiti yathu. Conco, musazengeleze kutumizila munthu wacidwi linki ya tsamba loyamba la webusaiti yathu kapena ya nkhani inayake pa tsambalo, kapenanso ya vidiyo ili pamenepo.