September 11-17
ESITERE 3-5
Nyimbo 85 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Thandizani Ena Kucita Zonse Zimene Angathe Potumikila Yehova”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
Esitere 4:12-16—Kodi timamenyela bwanji ufulu wathu wa kulambila monga anacitila Esitere na Moredekai? (kr 160 ¶14)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno ni mfundo iti yokupindulilani imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) Esitere 3:1-12 (th phunzilo 2)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwelelako: (Mph. 5) Kukambilana. Onetsani vidiyo yakuti Ulendo Wobwelelako: Ufumu—Mat 14:19, 20. Nthawi zonse vidiyo ikaima, inunso iimitseni na kufunsa omvela mafunso amene aonekela.
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 3) Makambilano anu atsamile pa mfundo yaikulu ya makambilani acitsanzo. M’fotokozeleni mmene phunzilo la Baibo limacitikila, na kumusiyila kakhadi kofunsila phunzilo la Baibo. (th phunzilo 16)
Phunzilo la Baibo: (Mph. 5) lff phunzilo 12 ndime yoyamba komanso mfundo 1-3 (th phunzilo 15)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Khala Bwenzi la Yehova—Esitere Anali Wolimba Mtima: (Mph. 5) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi. Ndiyeno ngati n’kotheka, funsani ana amene munawasankhilatu funso ili: Kodi ungakonde kutengela kulimba mtima kwa Esitere m’njila iti?
Zofunikila za Mpingo: (Mph. 10)
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lff phunzilo 57
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 125 na Pemphelo