CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Thandizani Ena Kucita Zonse Zimene Angathe Potumikila Yehova
Moredekai anapeleka citsanzo cabwino pa nkhani yokhala wolimba mtima komanso wokhulupilika kwa Yehova (Esitere 3:2-4; it-2 431 ¶7)
Iye anathandiza Esitere kuona zimene akanacita pothandiza anthu ake (Esitere 4:7, 8; it-2 431 ¶9)
Analimbikitsa Esitere kukhala wolimba mtima na kudalila Yehova (Esitere 4:12-14; ia 133 ¶22-23)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi zocita na zokamba zanga zimalimbikitsa ena mumpingo kucita zonse zimene angathe potumikila Yehova?’