Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Abusa Amene Amagwila Nchito Yothandiza Anthu a Yehova

Abusa Amene Amagwila Nchito Yothandiza Anthu a Yehova

Anthu ambili sakhulupilila anthu a paudindo. Ndipo m’pomveka cifukwa kuyambila kale-kale anthu ambili a paudindo akhala akugwilitsa nchito udindo wawo mwadyela. (Mika 7:3) Koma ife ndife oyamikila kwambili kuti akulu mumpingo amaphunzitsidwa kugwilitsa nchito udindo wawo pothandiza anthu a Yehova.—Esitere 10:3; Mat. 20:​25, 26.

Mosiyana na anthu a paudindo a m’dzikoli, abale amayesetsa kuti akhale oyang’anila cifukwa cokonda Yehova na anthu ake. (Yoh. 21:16; 1 Pet. 5:​1-3) Motsogoledwa na Yesu, abusa amenewa amathandiza wofalitsa aliyense kukhalabe pa ubwenzi wolimba na Yehova komanso kudzimva kuti ali m’banja la olambila ake. Iwo sazengeleza kupeleka thandizo lauzimu ku nkhosa za Yehova. Komanso amacitapo kanthu mofulumila ngati wina akufunika thandizo la zacipatala mwamsanga kapena ngati pagwa tsoka linalake. Ngati mufunika thandizo, khalani womasuka kukamba na mkulu aliyense mumpingo mwanu kapena kum’tumila foni.—Yak. 5:14.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI AKULU AMENE AMASAMALILA NKHOSA, KENAKO YAKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi Mariana anapindula bwanji na thandizo la akulu?

  • Kodi Elias anapindula bwanji na thandizo la akulu?

  • Pambuyo potamba vidiyoyi, kodi tsopano muiona bwanji nchito imene akulu amagwila?