Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

September 2-8

MASALIMO 79-81

September 2-8

Nyimbo 29 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Onetsani Kuti Mumakonda Dzina la Yehova la Ulemelelo

(Mph. 10)

Pewani kucita zinthu zosalemekeza Yehova (Sal. 79:9; w17.02 9 ¶5)

Muziitana pa dzina la Yehova (Sal. 80:18; ijwbv 3 ¶4-5)

Yehova amaŵadalitsa kwambili anthu amene amaonetsa cikondi pa dzina lake mwa kukhala omvela (Sal. 81:13, 16)

Kuti zocita zathu zilemekeze dzina la Yehova, tiyenela kudzidziŵikitsa kuti ndife Mboni zake

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 80:1​—N’cifukwa ciyani nthawi zina dzina la Yosefe linali kugwilitsidwa nchito pochula mtundu wonse wa Isiraeli? (it-2-E 111)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 79:1–80:7 (th phunzilo 10)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 1) KUNYUMBA NA NYUMBA. M’pempheni kuti muziphunzila naye Baibo. (lmd phunzilo 4 mfundo 4)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. M’pempheni kuti muziphunzila naye Baibo. (lmd phunzilo 4 mfundo 3)

6. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 2) ULALIKI WAPOYELA. M’pempheni kuti muziphunzila naye Baibo. (lmd phunzilo 3 mfundo 3)

7. Kubwelelako

(Mph. 5) KUNYUMBA NA NYUMBA. Pemphani munthu amene anakana kuphunzila m’mbuyomu kuti muyambe kuphunzila naye Baibo. (lmd phunzilo 8 mfundo 3)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 10

8. “Iwo Adzayeletsa Dzina Langa”

(Mph. 15) Kukambilana.

Satana anayamba kuipitsa dzina la Yehova m’munda wa Edeni. Kucokela pa nthawiyo, anthu onse komanso angelo amafunika kupanga cisankho pa nkhani yofunika kwambili, yakuti kaya adzayeletsa dzina la Yehova kapena ayi.

Onani mabodza ena amkunkhuniza amene Satana amafalitsa ponena za Yehova. Iye amati Yehova ni wolamulila wankhanza komanso wopanda cikondi. (Gen. 3:1-6; Yobu 4:18, 19) Amanenanso kuti alambili a Yehova samukonda na mtima wonse. (Yobu 2:4, 5) Iye wapangitsanso anthu mamiliyoni kukhulupilila kuti Yehova si ndiye Mlengi wa cilengedwe cokongola cimene timaona.​—Aroma 1:20, 21.

Kodi mabodza amenewa amakupangitsani kumva bwanji? N’kutheka kuti mumafuna kucitapo kanthu mwa kukhalila kumbuyo dzina la Yehova! Iye anali kudziŵa kuti anthu ake adzafuna kuthandiza pa kuyeletsa dzina lake. (Yelekezelani na Yesaya 29:23.) Kodi mungathandize bwanji?

  • Muzithandiza ena kum’dziŵa Yehova na kum’konda. (Yoh. 17:25, 26) Muzikhala okonzeka kupeleka umboni wakuti iye alikodi, ndipo muziphunzitsa ena za makhalidwe ake ocititsa cidwi.​—Yes. 63:7

  • Muzikonda Yehova na mtima wanu wonse. (Mat. 22:37, 38) Muzimvela malamulo a Yehova cifukwa cofuna kumukondweletsa, osati cabe cifukwa cakuti ni abwino kwa inu.​—Miy. 27:11

Tambitsani VIDIYO YAKUTI Cikondi Sicitha Olo Kuti . . . Anzanu ku Sukulu Ali na Makhalidwe Oipa. Kenako funsani omvela kuti:

  • Ni motani mmene Ariel na Diego anakhalila kumbuyo dzina la Yehova?

  • N’ciyani cinaŵalimbikitsa kukhalila kumbuyo dzina la Yehova?

  • Kodi mungatengele bwanji citsanzo cawo?

9. Phunzilo la Baibo la Mpingo

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 90 na Pemphelo