Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

October 21-27

MASALIMO 100-102

October 21-27

Nyimbo 37 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Onetsani Kuti Mumayamikila Cikondi Cosasintha ca Yehova

(Mph. 10)

Kulitsani cikondi canu pa Yehova (Sal. 100:5; w23.03 12 ¶18-19)

Pewani zinthu zimene zingawononge ubale wanu na Yehova (Sal. 101:2, 3; w23.02 17 ¶10)

Pewani anthu amene amaipitsa dzina la Yehova na gulu lake (Sal. 101:5; w11-CN 7/15 16 ¶7-8)

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi zina zimene nimacita poseŵenzetsa soshomidiya zingawononge ubale wanga na Yehova?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 102:6​—N’cifukwa ciyani wamasalimo anadziyelekezela na mbalame yochedwa vuwo? (it-2-E 596)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 102:1-28 (th phunzilo 12)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) KUNYUMBA NA NYUMBA. (lmd phunzilo 2 mfundo 3)

5. Kubwelelako

(Mph. 5) KUNYUMBA NA NYUMBA. M’pempheni kuti muyambe kuphunzila naye Baibo. (lmd phunzilo 9 mfundo 4)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila

(Mph. 4) Citsanzo. ijwbq 129​—Mutu: Kodi Baibo Anaisintha Kapena Anangoisinthako Zina? (th phunzilo 8)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 137

7. ‘Nakulondolani Kulikonse; Ndipo Inu Mwanigwila mwa Mphamvu’

(Mph. 15)

Kukambilana. Tambitsani VIDIYO. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi Anna anaonetsa bwanji cikondi cosasintha?

  • Nanga tingatengele bwanji citsanzo cake?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 17 ¶1-7

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 96 na Pemphelo