Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

October 7-13

MASALIMO 92-95

October 7-13

Nyimbo 84 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Kutumikila Yehova Ndiwo Umoyo Wabwino Koposa!

(Mph. 10)

Yehova ni woyenela kulambilidwa (Sal. 92:1, 4; w18.04 26 ¶5)

Iye amapatsa anthu ake luso la kuzindikila (Sal. 92:5; w18.11 20 ¶8)

Iye amakonda anthu amene amamutumikila ngakhale mu ukalamba wawo (Sal. 92:12-15; w20.01 19 ¶18)

DZIFUNSENI KUTI, ‘N’ciyani cikunilepheletsa kudzipatulila kwa Yehova na kubatizika?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal 92:5​—N’cifukwa ciyani tinganene kuti mawu awa afotokoza bwino nzelu za Yehova? (cl-CN 176 ¶18)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 94:1-23 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Pokambilana na munthu pezani njila yomuthandizila kudziŵa zimene mumacita monga mphunzitsi wa Baibo. (lmd phunzilo 5 mfundo 3)

5. Kubwelelako

(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. Yambitsani phunzilo la Baibo kwa munthu amene pa nthawi ina anakana kuphunzila. (lmd phunzilo 8 mfundo 4)

6. Kupanga Ophunzila

(Mph. 5) Kambilanani na wophunzila amene sakupita patsogolo. (lmd phunzilo 12 mfundo 5)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 5

7. Acicepele Akakhala na Nkhawa Yaikulu

(Mph. 15) Kukambilana.

Ifenso atumiki a Yehova timakhala na nkhawa. Mwacitsanzo, Davide anali kukhala na nkhawa nthawi zina, ndipo ni mmenenso zilili kwa abale athu ambili masiku ano. (Sal. 13:2; 139:23) N’zacisoni kuti ngakhale acicepele amavutika na nkhawa. Nthawi zina, nkhawa ingacititse wacicepele kuona zinthu zimene amacita nthawi zonse kukhala zovuta, monga kupita kusukulu kapena kupezeka ku misonkhano ya mpingo. Nthawi zinanso, ingamupangitse kukhala na mantha aakulu kapena maganizo ofuna kudzipha.

Acicepele, mukapanikizika cifukwa ca nkhawa, uzan’koni makolo anu kapena munthu wina wokhwima maganizo. Musaiŵalenso kupempha Yehova kuti akuthandizeni. (Afil. 4:6) Iye adzakuthandizani. (Sal. 94:17-19; Yes 41:10) Ganizilani citsanzo ca m’bale Steing.

Tambitsani VIDIYO YAKUTI Yehova Amanikonda. Kenako funsani omvela kuti:

• Ni lemba liti linathandiza m’bale Steing? Nanga n’cifukwa ciyani?

• Kodi Yehova anamuthandiza bwanji?

Inu makolo, thandizani ana anu kucepetsa nkhawa mwa kuŵamvetsela moleza mtima, kuŵaonetsa cikondi, komanso kuŵathandiza kukhulupilila kuti Yehova amaŵakondadi. (Tito 2:4; Yak. 1:19) Dalilani Yehova kuti akupatseni mphamvu n’colinga coti muzitha kulimbikitsa ana anu.

Nthawi zina sitingadziŵe kuti wina wake mu mpingo ali na nkhawa yaikulu, kapena sitingamvetse mmene akumvela. Ngakhale n’telo, tingathandizebe mwa kuonetsa cikondi kwa onse mu mpingo komanso kuwaona kuti ni ofunika.​—Miy. 12:25; Aheb. 10:24.

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 81 na Pemphelo