Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

September 16-22

MASALIMO 85-87

September 16-22

Nyimbo 41 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Pemphelo Limatithandiza Kupilila

(Mph. 10)

Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kukhala wacimwemwe (Sal. 86:4)

Muzim’pempha kuti akuthandizeni kukhalabe wokhulupilika (Sal. 86:11, 12; w12-CN 5/15 25 ¶10)

Muzikhulupilila kuti Yehova adzayankha mapemphelo anu (Sal. 86:6, 7; w23.05 13 ¶17-18)


DZIFUNSENI KUTI, ‘Nikakhala na mavuto, kodi nimapeleka mapemphelo otalikilapo komanso kaŵili-kaŵili?’​—Sal. 86:3.

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 86:11​—Kodi pemphelo la Davide lionetsa ciyani ponena za mtima wa munthu? (it-1-E 1058 ¶5)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 86:1–87:7 (th phunzilo 12)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. M’pempheni kuti muziphunzila naye Baibo. (lmd phunzilo 3 mfundo 5)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Kambilanani na munthu amene pa makambilano apita anakamba kuti ali na nkhawa cifukwa ca zina zake zimene zikucitika, ndipo m’pempheni kuti muziphunzila naye Baibo. (lmd phunzilo 7 mfundo 4)

6. Kupanga Ophunzila

(Mph. 5) lff phunzilo 15 mfundo 5. Kambilanani makonzedwe amene mwapanga kuti wophunzila wanu akaphunzilebe mlungu wotsatila ngakhale kuti mudzacokapo. (lmd phunzilo 10 mfundo 4)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 83

7. Musaleke Kulalikila

(Mph. 5.) Kukambilana.

Tambitsani VIDIYO. Kenako funsani omvela kuti:

  • N’cifukwa ciyani nthawi zina tingaganize zongoleka kulalikila?

  • Nanga n’cifukwa ciyani sitiyenela kuleka?

8. Musaleke Kuyambitsa Maphunzilo a Baibo!

(Mph. 10) Kukambilana.

Kodi mwayambitsako phunzilo la Baibo poseŵenzetsa bulosha ya Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! pa kampeni yapadela imene tili nayo mwezi uno? Ngati n’conco, mosakayikila ndinu wokondwela ngako! N’kuthekanso kuti abale na alongo ena alimbikitsidwa cifukwa munayambitsa phunzilo la Baibo. Koma ngati mukalibe kuyambitsako phunzilo la Baibo, mungayambe kuganiza kuti khama lanu lapita pacabe. Kodi mungacite ciyani ngati mwayamba kufooka cifukwa simunayambitseko phunzilo la Baibo?

Tambitsani VIDIYO YAKUTI “Timasonyeza Kuti Ndife Atumiki a Mulungu . . . Mwa Kukhala Oleza Mtima”​—Pamene Tilalikila. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi 2 Akorinto 6:4, 6 ingatithandize bwanji tikayamba kuganiza kuti utumiki wathu ukupita pacabe?

  • Kodi mungapange masinthidwe otani mukayamba kuganiza kuti khama lanu poyambitsa phunzilo la Baibo lapita pacabe?

Muzikumbukila kuti cimwemwe cathu sicidalila pa maphunzilo a Baibo amene tayambitsa kapena amene timatsogoza. Koma timakhala na cimwemwe podziŵa kuti Yehova amasangalala na khama lathu. (Luka 10:17-20) Conco pitilizani kutengako mbali mokwanila pa kampeni yapadela imeneyi, podziwa kuti “zonse zimene mukucita pa nchito ya Ambuye sizidzapita pacabe”!​—1 Akor. 15:58.

9. Phunzilo la Baibo la Mpingo

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 39 na Pemphelo