Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

September 30–October 6

MASALIMO 90-91

September 30–October 6

Nyimbo 140 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Muzidalila Yehova Kuti Mukhale na Moyo Wautali

(Mph. 10)

Anthufe, palibe cimene tingacite kuti titalikitseko moyo wathu (Sal 90:10; wp19.3 5 ¶3-5)

Yehova ni “Mulungu kuyambila kalekale mpaka kalekale” (Sal 90:2; wp19.1 5, bokosi)

Iye sadzalephela kupeleka moyo wosatha kwa onse amene amamudalila (Sal 21:4; 91:16)

Musawononge ubale wanu na Yehova mwa kulandila cithandizo ca mankhwala cosagwilizana na mfundo zake.​—w22.06 18 ¶16-17.

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal 91:11​—Kodi tiyenela kuliona motani thandizo la angelo? (wp17.5 5)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal 91:1-16 (th phunzilo 10)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. Popanda kufotokoza mfundo ya m’Baibo, thandizani mwininyumba kukhala womasuka kufotokoza zimene zimam’detsa nkhawa n’colinga cakuti mudziŵe mmene Baibo ingam’thandizile kukhala na umoyo wabwino. (lmd phunzilo 1 mfundo 3)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. (lmd phunzilo 1 mfundo 4)

6. Nkhani

(Mph. 5) lmd zakumapeto A mfundo 5​—Mutu: Mukhoza kudzakhala na moyo kwamuyaya pa dziko lapansi. (th phunzilo 14)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 158

7. Muziyamikila Ubwino wa Kuleza Mtima Kwakukulu kwa Yehova​—M’mene Yehova Amaonela Nthawi

(Mph. 5) Kukambilana.

Tambitsani VIDIYO. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi kuganizila mmene Yehova amaonela nthawi kungatithandize bwanji kuyembekezela malonjezo ake moleza mtima?

8. Vidiyo ya Zimene Gulu Lakwanitsa Kucita ya September

(Mph. 10) Tambitsani VIDIYO.

9. Phunzilo la Baibo la Mpingo

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 68 na Pemphelo