Ziŵelengelo Zonse za mu 2019
Nthambi za Mboni za Yehova: 87
Ciŵelengelo ca Maiko ocitila Lipoti: 240
Ciŵelengelo ca Mipingo yonse: 119,712
Opezeka pa Cikumbutso Padziko Lonse: 20,919,041
Amene Anadya Ziphiphilitso Padziko Lonse: 20,526
Ofalitsa Onse Amene Anagwila Nchito Yolalikila *: 8,683,117
Avaleji ya Ofalitsa Amene Anali kulalikila Mwezi Uliwonse: 8,471,008
Kuwonjezeka kwa Ofalitsa Kucokela mu 2018: 1.3%
Onse Amene Anabatizika *: 303,866
Avaleji ya Apainiya * Mwezi Uliwonse: 1,277,738
Avaleji ya Apainiya Othandiza Mwezi Uliwonse: 464,980
Maola Onse Amene Tinathela Mu Utumiki: 2,088,560,437
Avaleji ya Maphunzilo a Baibo * Mwezi Uliwonse: 9,618,182
M’caka ca utumiki ca 2019, * Mboni za Yehova zinagwilitsa nchito ndalama zoposa madola 224 miliyoni posamalila apainiya apadela, amishonale komanso oyang’anila madela pa utumiki wawo. ▪ Padziko lonse pali abale na alongo okwana 20,858, amene akutumikila m’maofesi a nthambi. Onse amenewa ali m’Gulu Lapadziko Lonse la Atumiki Apadela a Nthawi Zonse a Mboni za Yehova.
^ ndime 7 Wofalitsa ni munthu amene amalalikila mwakhama uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Kuti mudziŵe mmene timapezela ciŵelengelo cimeneci, onani nkhani yakuti “Kodi a Mboni za Yehova Alipo Angati Padziko Lonse?” pa jw.org ku chichewa
^ ndime 10 Kuti mudziŵe zimene mungacite kuti mubatizidwe n’kukhala wa Mboni za Yehova, onani nkhani yakuti “Kodi Ndingatani Kuti Ndikhale wa Mboni za Yehova?” pa jw.org ku chichewa.
^ ndime 11 Mpainiya ni wa Mboni wacitsanzo cabwino amene amadzipeleka kuti azilalikila uthenga wabwino kwa maola ena ake mwezi uliwonse.
^ ndime 14 Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani ya pa jw.org yakuti “Kodi Phunzilo la Baibulo N’ciani?”
^ ndime 15 Caka ca utumiki ca 2019 cinayamba pa September 1, 2018, ndipo cinasila pa August 31, 2019.