Gao 3
Kucokela Pamene Mulungu Anapulumutsa Aisiraeli ku Iguputo, Kukafika pa Mfumu Yao Yoyamba
Mose anatsogolela Aisiraeli kucokela ku Iguputo kumene anali akapolo, kupita nao ku phili la Sinai. Kumeneko Mulungu anawapatsa malamulo ake. Pambuyo pake, Mose anatuma amuna 12 kuti akaone dziko la Kanani. Koma pamene anabwelako, amuna 10 aja anakamba vinthu voipa cabe ponena za dziko la Kanani. Iwo anacititsa kuti anthu afune kubwelela ku Iguputo. Cifukwa cakuti Aisiraeli analibe cikhulupililo, Mulungu anawapatsa cilango, cakuti anawayendetsa mozungulila mu cipululu kwa zaka 40.
Potsilizila pake, Yoswa anasankhidwa kuti atsogolele Aisiraeli ndi kuloŵa nao mu dziko la Kanani. Pofuna kuwathandiza kulanda dziko limenelo, Yehova anacita zozizwitsa. Anaimitsa madzi a mtsinje wa Yorodano, anagwetsa zipupa za Yeriko, ndipo anaimitsa dzuŵa kuti lisayende tsiku lonse. Pambuyo pazaka 6, Aisiraeli analanda Akanani dziko lao.
Kuyambila pa Yoswa, oweluza ndio anali kulamulila Aisiraeli kwa zaka 356. Tidzaphunzila za ambili a io, kuphatikizapo Baraki, Gidiyoni, Yefita, Samsoni ndi Samueli. Ndiponso tidzaŵelenga za akazi ena monga Rahabi, Debora, Yaeli, Rute, Naomi ndi Delila. Gao 3 lonse limafotokoza zimene zinacitika pazaka 396.