Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 48

Agibeoni Anzelu

Agibeoni Anzelu

ANTHU m’mizinda yambili ya ku Kanani akonzekela kucita nkhondo ndi Aisiraeli. Iwo aganiza kuti angawine nkhondo. Koma anthu a mu mzinda wapafupi wa Gibeoni aona kuti sangawine. Iwo akhulupilila kuti Mulungu athandiza Aisiraeli. Conco safuna kuti amenyane ndi Mulungu. Kodi udziŵa cimene Agibeoni acita?

Iwo adzipanga kuoneka monga acokela kutali kwambili. Avala zovala zong’ambika-ng’ambika ndi nsapato zakutha. Akwezeka masaka ao akutha pa abulu, kapena kuti pa madonki, ndipo anyamula mkate wouma umene wakhala nthawi yaitali. Ndiyeno apita kwa Yoswa ndi kumuuza kuti: ‘Ife tacokela ku dziko lakutali, cifukwa tamva kuti Mulungu wanu, Yehova ni wamkulu. Tinamva zinthu zimene anakucitilani ku Iguputo. Conco, atsogoleli athu anatiuza kuti titenge zakudya ndi kukonzekela ulendo kubwela kuno kudzakupemphani kuti: “Ife ndife akapolo anu. Lonjezani kuti simudzacita nkhondo ndi ife.” Onani zovala zathu kung’ambika-ng’ambika cifukwa ca ulendo wautali, ndipo mkate wathu wakhala nthawi yaitali ndipo unauma.’

Yoswa ndi atsogoleli anzake akhulupilila Agibeoni. Conco, awalonjeza kuti sadzacita nao nkhondo. Koma patapita cabe masiku atatu, io adziŵa kuti Agibeoni amakhala pafupi.

Yoswa awafunsa kuti: ‘N’cifukwa ciani munatiuza kuti munacokela ku dziko la kutali?’

Agibeoni ayankha kuti: ‘Tinacita zimenezi cifukwa tinamva kuti Mulungu wanu, Yehova, anakulonjezani kuti adzakupatsani dziko lonse la Kanani. Conco, tinacita mantha kuti mudzatipha.’ Motelo, Aisiraeli asunga lonjezo lao ndipo sakupha Agibeoni. M’malo mwake, awatenga kukhala akapolo ao.

Mfumu ya Yerusalemu yakalipa kwambili cifukwa cakuti Agibeoni apangana za mtendele ndi Aisiraeli. Conco, iuza mafumu ena 4 kuti: ‘Bwelani kuno mutithandize kucita nkhondo ndi Agibeoni.’ Izi n’zimene mafumu awa 5 acita. Kodi Agibeoni anacita bwino kupangana za mtendele ndi Aisiraeli, zimene zacititsa mafumu awa kumenyana nao? Tiye tione.

Yoswa 9:1-27; 10:1-5.