Nkhani 50
Akazi Aŵili Olimba Mtima
AISIRAELI ali pamavuto, ndipo alilila Yehova kuti awathandize. Yehova awayankha mwa kuwapatsa atsogoleli opanda mantha kuti awathandize. Baibo imacha atsogoleli amenewa kuti oweluza. Yoswa anali woweluza woyamba ndipo pambuyo pake panabwela oweluza ena monga Otiniyeli, Ehudi ndi Samagara. Koma pakati pa anthu amene athandiza Aisiraeli, palinso akazi aŵili, Debora ndi Yaeli.
Debora ndi mneneli wacikazi. Yehova amamuuza za kutsogolo, ndipo iye amauza anthu zimene Yehova wakamba. Ndiponso Debora ndi woweluza. Iye amakhala pansi pa mtengo wa kanjedza mu dela la dziko la mapili Anthu amabwela kwa iye kuti apeze thandizo pa mavuto ao.
Panthawi imeneyi Yabini ndiye mfumu ya ku Kanani. Iye ali ndi magaleta ankhondo 900. Asilikali ake ndi amphamvu kwambili cakuti Aisiraeli ambili akhala akapolo ake. Sisera ndiye mtsogoleli wake wa nkhondo.
Tsiku lina Debora atumiza mau kwa woweluza Baraki ndi kumuuza kuti: ‘Yehova walamula kuti: “Tenga amuna 10,000 ndipo mukasonkhane paphili la Tabori. Pamenepo Ine ndidzabweletsa Sisera kwa iwe. Ndipo ndidzamupeleka m’manja mwako.”’
Baraki auza Debora kuti: ‘N’dzapita ngati iwe udzapita ndi ine.’ Conco Debora ayendela pamodzi ndi Baraki, koma auza Baraki kuti: ‘Iwe sudzalandila ulemelelo wa kupambana nkhondo, cifukwa Yehova adzapeleka Sisera m’manja mwa mkazi.’ Ndipo izi n’zimene zicitika.
Baraki aseluka mu phili la Tabori kuti amenyane ndi asilikali a Sisera. Mwadzidzidzi, Yehova acititsa madzi kusefukila, ndipo asilikali ambili a adani ambila m’madzi ndi kufa. Koma Sisera aseluka m’galeta lake ndi kuthaŵa.
Pamene athaŵa, Sisera afika kutenti ya mkazi wina, dzina lake Yaeli. Yaeli amulandila ndi kumupatsa mkaka kuti amwe. Pamene Sisera akumwa mkaka, amvela tulo, ndipo agona. Ndiyeno Yaeli atenga cimsomali cokhomela tenti ndi kukhokhomela kumutu kwa munthu woipa ameneyu. Pambuyo pake, Baraki afika ndipo Yaeli amuonetsa Sisera wakufa. Kodi waona kuti zimene Debora anakamba zacitika?
Potsilizila pake, nayo Mfumu Yabini iphedwa, ndipo Aisiraeli akhalanso pamtendele kwa kanthawi.
Oweruza 2:14-22; 4:1-24; 5:1-31.