Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 42

Bulu Akamba

Bulu Akamba

KODI unamvelapo bulu, kapena kuti donki, kukamba? Ungakane kuti ‘Iyai bulu sakamba. Nyama sizikamba.’ Koma Baibo imatiuza za bulu amene anakamba. Tiye tione mmene zinacitikila.

Aisiraeli atsala pang’ono kuloŵa mu dziko la Kanani. Mfumu ya ku Moabu, Balaki, ili ndi mantha kuopa Aisiraeli. Conco, yaitana munthu wocenjela, Balamu, kuti atembelele Aisiraeli. Balaki alonjeza Balamu kuti adzamupatsa ndalama zambili. Conco Balamu anyamuka ulendo pabulu kupita kwa Balaki.

Yehova safuna kuti Balamu akatembelele anthu ake. Conco atumiza mngelo amene ali ndi lupanga lalitali kukaima panjila kuti amuchingilize. Balamu saona kuti kutsogolo kuli mngelo, koma bulu waona. Poona izi, buluyo ayesa-yesa kuti apewe mngelo, ndipo potsilizila pake angokhala pansi. Balamu akalipa kwambili cakuti amenya bulu ndi ndodo yake.

Ndiyeno Yehova acititsa Balamu kumvela bulu wake akukamba naye. Bulu afunsa kuti: ‘Nanga nakulakwilani ciani kuti munimenye conco?’

Balamu ayankha kuti: ‘Wanipangitsa kukhala monga citsilu. Ngati panali lupanga n’kanakuphelatu!’

Bulu afunsa kuti: ‘Kodi n’nacitapo za conco?’

Balamu ayankha kuti: ‘Iyai.’

Pamenepo Yehova atsegula maso a Balamu ndipo aona mngelo ali kutsogolo ndi lupanga. Mngeloyo akamba kuti: ‘N’cifukwa ciani umenya bulu wako conco? Ndabwela kudzakuletsa kuti usakatembelele Aisiraeli. Ngati bulu wako sanandipewe, ndikanakupha, ndipo bulu wako ndikanamusiya wamoyo.’

Pamene Balamu amvela izi akuti: ‘Ndacimwa. Sin’nadziŵe kuti mwaima panjila.’ Ndiyeno mngelo amusiya kuti apite. Balamu apitiliza ulendo wake kukaonana ndi Balaki. Iye afunitsitsa kuti mpaka akatembelele Aisiraeli. Koma m’malo mwake, Yehova amucititsa kuti adalitse Aisiraeli katatu.

Numeri 21:21-35; 22:1-40; 23:1-30; 24:1-25.