Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 55

Kamnyamata Kotumikila Mulungu

Kamnyamata Kotumikila Mulungu

ONA kamnyamata kukongola! Dzina lake ni Samueli. Ndipo mwamuna amene akagwila pamutu ni Eli, mkulu wa ansembe wa Aisiraeli. Ena amene uona pacithunzi-thunzi apa ni Elikana atate a Samueli, ndi Hana amai ake. Iwo abweletsa Samueli kwa Eli.

Panthawi imeneyi, Samueli ali cabe ndi zaka zinai kapena zisanu. Ndiyeno amupeleka kuti akakhale ku cihema ca Yehova ndi Eli, pamodzi ndi ansembe ena. Nanga n’cifukwa ciani Elikana ndi Hana apeleka mwana mng’ono conco kuti akatumikile Yehova pa cihema? Tiye tione.

Pamene kunatsala zaka zocepa cabe kuti zimenezi zicitike, Hana anali wacisoni kwambili, cifukwa cakuti analibe mwana. Koma anali kufunitsitsa kwambili kukhala ndi mwana. Conco, tsiku lina pamene Hana anali ku cihema ca Yehova, anapemphela kuti: ‘Yehova, musaniiwale! Ngati mudzanipatsa mwana mwamuna, nilonjeza kuti Nidzamupeleka kwa inu kuti akakutumikileni moyo wake wonse.’

Yehova anayankha pemphelo la Hana, ndipo patapita miyezi, Hana anabala Samueli. Anali kukonda kwambili mwana wake, ndipo anayamba kumuphunzitsa za Yehova pamene anali kamwana kwambili. Anauza mwamuna wake kuti: ‘Mwana uyu akaleka cabe kunyonkha, Nidzamupeleka ku cihema ca Yehova kuti akatumikile Yehova kumeneko.’

Izi n’zimene Hana ndi Elikana acita pacithunzi-thunzi apa. Cifukwa cakuti Samueli anaphunzitsidwa bwino ndi makolo ake, anali wokondwela kutumikila pa tenti ya Yehova. Caka ciliconse, Hana ndi Elikana anali kuyenda kukalambila ku tenti yapadela imeneyi, ndi kukacezela mwana wao. Ndiyeno caka ciliconse, Hana anali kupeleka malaya odula manja amene anali kupangila Samueli.

Pamene zaka ziyenda, Samueli apitiliza kutumikila pa cihema ca Yehova, ndipo Yehova ndi anthu amukonda Samueli. Koma Hofeni ndi Pinihasi, ana a Eli mkulu wansembe, si anthu abwino. Amacita vinthu voipa kwambili, ndipo amacititsa anthu ena kusamvela Yehova. Eli ayenela kuwacotsa pa kukhala ansembe koma sacita zimenezi.

Samueli safuna kuti aleke kutumikila Yehova cifukwa ca vinthu voipa vimene vicitika ku cihema. Cifukwa cakuti ni anthu ang’ono amene akonda Yehova, papita nthawi pamene Yehova analankhula ndi munthu. Pamene Samueli akulako pang’ono, izi n’zimene zicitika:

Pamene Samueli aligone mu cihema, amvela kuitana. Agalamuka ndi kuyankha kuti: ‘Ndine pano.’ Ndipo anyamuka ndi kuthamangila kwa Eli kukamuuza kuti: ‘Mwaniitana, nabwela.’

Koma Eli ayankha kuti: ‘Sininakuitane mwana wanga, yenda ukagone.’ Pamenepo Samueli abwelela kukagona.

Koma aitanidwanso kaciŵili kuti: ‘Samueli’! Samueli aukanso ndi kuthamangila kwa Eli. Amuuzanso kuti: ‘Mwaniitana, nabwela.’ Koma Eli ayankha kuti: ‘Sindinakuitane mwana wanga, pita ukagone.’ Samueli abwelelanso kukagona.

Ndipo liu limvekanso kacitatu kuti: ‘Samueli’! Samueli athamangilanso kwa Eli. Ndipo akamba kuti: ‘Nabwela, cifukwa apa mwandiitana zoona.’ Tsopano Eli adziŵa kuti Yehova ndi amene aitana Samueli. Conco auza Samueli kuti: ‘Pita ukagonenso, ndipo akaitananso, ukambe kuti: “Kambani Yehova, popeza mtumiki wanu akumvetsela.”’

Izi n’zimene Samueli acita pamene Yehova aitananso. Yehova auza Samueli kuti adzapeleka cilango kwa Eli ndi ana ake. Pambuyo pake, Hofeni ndi Pinihasi anafa m’nkhondo yomenyana ndi Afilisti, ndipo pamene Eli akumva zimenezi akugwa pansi ndi kuthyola khosi ndi kufa. Conco mau a Yehova akwanilitsika.

Samueli akhala woweluza wotsilizila wa Aisiraeli. Pamene akula anthu amuuza kuti: ‘Tisankhile mfumu izitilamulila.’ Samueli safuna kucita zimenezi, cifukwa Yehova ndiye mfumu yao. Koma Yehova amuuza kuti amvele zimene anthu amupempha.

1 Samueli 1:1-28; 2:11-36; 4:16-18; 8:4-9.