Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 47

Kawalala Mu Isiraeli

Kawalala Mu Isiraeli

KODI waona cimene mwamuna uyu afocela mu tenti yake? Iye afocela covala cokongola, golide, ndi ndalama zasiliva. Wazitenga ku mzinda wa Yeriko. Kodi zinthu za ku Yeriko afunikila kucita nazo ciani? Kodi ukumbukila?

Afunikila kuziononga, ndipo golide ndi siliva ayenela kuzipeleka ku cipinda cosungilako cuma mu cihema ca Yehova. Conco anthu awa sanamvele Mulungu. Abela Mulungu. Dzina la munthu uyu ni Akani, ndipo anthu amene ali naye ndi banja lake. Tiye tione cimene cicitika.

Pambuyo pakuti Akani waba zinthu zimenezi, Yoswa atuma amuna kuti akacite nkhondo ndi mzinda wa Ai. Koma io aluza pankhondo imeneyo. Ena aphedwa, ndipo ena athaŵa. Yoswa ali ndi cisoni kwambili. Iye adzigwetsela pansi ndi kupemphela kwa Yehova kuti: ‘N’cifukwa ciani mwalola zimenezi kucitika?’

Yehova ayankha kuti: ‘Nyamuka! Aisiraeli acimwa. Atenga zinthu zofunika kuonongedwa kapena kupelekedwa ku cihema ca Yehova. Aba ndi kubisa covala cokongola. Sinidzakudalitsani mpaka muononge zinthu zimenezi pamodzi ndi munthu amene wazitenga.’ Yehova auza Yoswa kuti adzamuonetsa munthu woipa ameneyo.

Conco Yoswa asonkhanitsa anthu onse, ndipo Yehova amuonetsa munthu woipa uja Akani. Akani akamba kuti: ‘Ndacimwa. Ndinaona covala cokongola, ndi golide ndi ndalama zasiliva. N’nazikhumbila ndipo n’nazitenga. Mudzazipeza zofocela pansi mu tenti yanga.’

Pamene apeza zinthu zimenezi ndi kuzipeleka kwa Yoswa, iye auza Akani kuti: ‘N’cifukwa ciani watibweletsela mavuto? Iwenso Yehova adzakubweletsela mavuto!’ Pamenepo anthu onse atema miyala Akani ndi banja lake mpaka kufa. Zimenezi zitiphunzitsa kuti sitiyenela kutenga zinthu zimene sizili zathu, si conco?

Pambuyo pake Aisiraeli abwelelanso kukacita nkhondo ndi mzinda wa Ai. Apa tsopano Yehova athandiza anthu ake, ndipo io awina nkhondo.

Yoswa 7:1-26; 8:1-29.