Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 46

Mpanda Wa Yeriko

Mpanda Wa Yeriko

A-AA! N’ciani cagwetsa mpanda, kapena kuti cipupa ca Yeriko? Cioneka monga pagwela bomba. Koma panthawi iyi mabomba ndi mfuti kunalibe. Ici n’cozizwitsa cina. Tiye tione mmene zinacitikila.

Yehova auza Yoswa kuti: ‘Iwe ndi asilikali ako muyende kuzungulila mzinda. Muuzungulile kamodzi patsiku kwa masiku 6. Munyamule likasa la cipangano. Ansembe 7 aziyenda kutsogolo kwa likasa ndi kuliza malipenga ao.

‘Patsiku la 7 mukazungulile mzindawo maulendo 7. Ndiyeno mukalize malipenga mosalekeza ndipo aliyense akafuule mfuu ya nkhondo. Pamenepo mpanda wonse unaundumuka kuti wuu pansi!’

Yoswa ndi anthu acita zimene Yehova wakamba. Pamene azungulila mzinda aliyense ali zii! osakamba ciliconse. Kunali kumveka cabe kulila kwa malipenga ndi mgugu wa miyendo. Zimenezi zicititsa mantha adani a Mulungu mu Yeriko. Kodi waiona nthambo yofiila imene ioneka pawindo apo? Kodi ni windo ya ndani imeneyi? Inde, Rahabi wacita zimene azondi aŵili aja anamuuza. Iye ndi acibanja ake ali mu nyumba ndipo aona zimene zicitika.

Ndiyeno patsiku la 7, pambuyo pakuti azungulila mzinda mauledo 7, aliza malipenga ndipo asilikali afuula. Pamenepo mpanda ukugwa. Ndiyeno Yoswa auza anthu kuti: ‘Muphe munthu aliyense mu mzinda ndi kuuwocha. Muwoche zinthu zonse. Koma, siliva, golide, mkuwa, ndi citsulo muzipeleke ku cipinda cosungilamo cuma kucihema ca Yehova.’

Ndiyeno Yoswa auza azondi aŵili aja kuti: ‘Pitani ku nyumba ya Rahabi, mumutulutse pamodzi ndi onse amene ali naye.’ Rahabi ndi acibanja ake apulumuka monga mmene azondi aja anakambila.

Yoswa 6:1-25.