Nkhani 36
Mwana Wa Ng’ombe Wagolide
A-AA! Kodi anthu awa acita ciani? Apemphela kwa mwana wa ng’ombe! N’cifukwa ciani acita zimenezi?
Pamene Mose akhala nthawi itali mu phili muja, anthu ayamba kukamba kuti: ‘Sitidziŵa zimene zacitika kwa Mose. Conco tiyeni tipange mulungu kuti atitsogolele kucoka mu dziko lino.’
Aroni mkulu wa Mose akamba kuti: ‘Cabwino, vulani masikiyo agolide mundipatse.’ Anthu aja amupatsa zimenezo, ndipo Aroni azisungunula ndi kupanga mwana wa ng’ombe wagolide. Pamenepo, anthu aja akamba kuti: ‘Uyu ndiye Mulungu wathu amene anaticotsa ku Iguputo.’ Conco Aisiraeli acita cikondwelelo cacikulu, ndipo alambila mwana wa ng’ombe wagolide.
Pamene Yehova aona zimenezi, akalipa kwambili, cakuti auza Mose kuti: ‘Fulumila seluka. Anthu acita cinthu coipa kwambili. Aiŵala malamulo anga ndipo ali kugwadila mwana wa ng’ombe wagolide.’
Mose aseluka msanga-msanga mu phili. Pamene afika pafupi, apeza kuti anthu aimba nyimbo ndi kuvina mozungulila mwana wa ng’ombe wagolide uja! Mose akalipa kwambili cakuti ataya pansi miyala iŵili ija imene pali malamulo, ndipo iphwanyika-phwanyika kukhala tuzidutswa mbwee pansi. Atenga mwana wa ng’ombe wagolide uja ndi kumusungunula. Ndiyeno amupela-pela kukhala monga unga.
Anthu acita cinthu coipa kwambili. Conco Mose auza amuna ena kutenga malupanga ao. Iye akuti: ‘Anthu oipa amene alambila mwana wa ng’ombe wagolide ayenela kufa.’ Ndipo amuna aja akupha anthu 3,000! Kodi izi si zionetsa kuti tifunika kusamala kuti tizilambila Yehova yekha, osati milungu ina yabodza?
Ekisodo 32:1-35.