Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 39

Ndodo Ya Aroni Imela Maluŵa

Ndodo Ya Aroni Imela Maluŵa

ONA maluŵa ndi zipatso zakupsa za maamondi zimene zamela kundodo. Imeneyi ni ndodo ya Aroni. Maluŵa aya ndi zipatso izi zakupsa zamela kundodo ya Aroni usiku umodzi cabe! Tiye tione cifukwa cake.

Aisiraeli akhala akuzungulila-zungulila mu cipululu kwa zaka zambili. Anthu ena safuna kuti Mose apitilize kukhala mtsogoleli, kapena Aroni kukhala mkulu wa ansembe. Kora ni amene aganiza zimenezi, kuphatikizapo Datani, Abiramu, ndi atsogoleli ena okwana 250. Anthu amenewa auza Mose kuti: ‘Nanga n’cifukwa ciani inu mumadzikweza pa anthu onse?’

Mose auza Kora ndi otsatila ake kuti: ‘Maŵa kum’maŵa mukatenge mapani ofukizila ndipo mukaikemo zofukiza. Ndiyeno mukabwele kucihema ca Yehova. Tidzaona amene Yehova adzasankha.’

Tsiku lotsatila Kora ndi otsatila ake 250 abwela kucihema. Anthu ena ambili naonso abwela kuti acilikize amuna amenewa. Yehova wakalipa kwambili. Mose auza anthu kuti: ‘Cokani kumatenti a anthu oipa awa, ndipo musagwile kanthu kao kalikonse.’ Anthu amvela ndi kucoka kumatenti a Kora, Datani, ndi Abiramu.

Ndiyeno Mose akamba kuti: ‘Mwa ici mudzadziŵa munthu amene Yehova adzasankha. Pansi padzatseguka ndi kumeza anthu oipa awa.’

Pamene Mose atsiliza cabe kukamba, pansi patseguka ndi kumeza tenti ya Kora ndi katundu wake wonse, komanso Datani ndi Abiramu kuphatikizapo onse amene ali nao. Pamene anthu amvela kulila kwa anthu amene amezedwa, io afuula kuti: ‘Tiyeni tithaŵe! nthaka ingatimeze!’

Panthawi imeneyi Kora ndi otsatila ake 250 akali pafupi ndi cihema. Conco Yehova atumiza moto, ndipo uwatentha onse. Ndiyeno, Yehova auza Eleazara, mwana wa Aroni, kuti atenge mapani ofukizila nsembe a amuna amene afa, kuti apangile lata lophimbila paguwa la nsembe. Lata lophimbila paguwa la nsembe limeneli ni cenjezo kwa Aisiraeli lakuti pasapezeke munthu aliyense, kusiyapo Aroni ndi ana ake, amene ayenela kukhala wansembe wa Yehova.

Koma Yehova afuna kuti anthu adziŵe kuti wasankha Aroni ndi ana ake kukhala ansembe. Conco auza Mose kuti: ‘Mtsogoleli aliyense wa fuko la Aisiraeli abweletse ndodo yake. Aroni abweletse ndodo ya fuko la Alevi. Ndiyeno uike ndodo zimenezi mu cihema kutsogolo kwa likasa la cipangano. Ndodo imene idzamela maluŵa idzaonetsa kuti mwini wake ni amene ndasankha kukhala wansembe.’

Tsiku lotsatila kum’mawa, Mose apita kucihema kuti akaone. Iye apeza kuti ndodo ya Aroni yamela maluŵa ndi zipatso za maamondi zakupsa! Kodi waona cifukwa cake Yehova anacititsa kuti ndodo ya Aroni imele maluŵa?

Numeri 16:1-49; 17:1-11; 26:10.