Nkhani 41
Njoka Yamkuwa
KODI njoka imene yapomba kumtengo iyi ioneka kuti ni ya zoona? Si ya zoona. Njoka iyi anaipanga ndi mkuwa, kapena kuti kopa. Yehova anauza Mose kuika njoka imeneyi kucimtengo kuti anthu akaiyang’ana asafe. Koma njoka izo zimene zili pansi n’za zoona. Zaluma anthu cakuti adwala. Kodi udziŵa cifukwa cake?
Cili cifukwa cakuti Aisiraeli akamba zoipa kwa Mulungu ndi Mose. Iwo adandaula kuti: ‘N’cifukwa ciani munaticotsa kudziko la Iguputo kuti tidzafele mu cipululu muno? Mulibe cakudya kapena madzi. Ndipo vimana ivi vatitinkha.’
Koma mana n’cakudya cabwino. Ndipo Yehova awapatsa cakudya cimeneci mozizwitsa. Awapatsanso madzi mozizwitsa. Koma anthu sayamikila Mulungu pa cisamalilo cimene awapatsa. Conco Yehova atumiza njoka za poizoni kuti ziwalange Aisiraeli. Njoka zawaluma ndipo anthu ambili afa.
Potsilizila pake, anthu apita kwa Mose ndi kumuuza kuti: ‘Tacimwa ife, cifukwa takamba zoipa kwa Yehova ndi imwe. Conde pemphelani kwa Yehova kuti aticotsele njoka izi.’
Conco Mose apemphela kwa Yehova. Ndiyeno Yehova auza Mose kuti apange njoka yamkuwa. Akamba kuti aiike pacimtengo kuti aliyense amene njoka yazoona yamuluma ayang’ane njoka yamkuwa. Mose acita zimene Mulungu wamuuza. Ndipo anthu amene alumidwa ayang’ana njoka yamkuwa imeneyi ndipo akhalanso bwino.
Pali phunzilo limene titengapo pa zimene zinacitika izi. Ife tonse, tili monga Aisiraeli amene analumidwa ndi njoka. Ndife oyenelela kufa. Kulikonse padziko lapansi anthu amakalamba, kudwala, ndi kufa. Zili conco cifukwa mwamuna ndi mkazi woyamba, Adamu ndi Hava, anacimwila Yehova, ndipo ife tonse ndife ana ao. Koma Yehova wakonza njila imene tingapezele moyo wamuyaya.
Yehova anatumiza Mwana wake, Yesu Kristu, padziko lapansi. Yesu anapacikidwa pamtengo, cifukwa cakuti anthu ambili anaganiza kuti iye anali munthu woipa. Koma Yehova anatumiza Yesu kuti adzatipulumutse. Ngati tiyang’ana kwa iye ndi kumutsatila, tidzapeza moyo wamuyaya. Koma tidzaphunzila zambili pa zimenezi mu nkhani za kutsogolo.
Numeri 21:4-9; Yohane 3:14, 15.