Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 35

Yehova Apeleka Malamulo Ake

Yehova Apeleka Malamulo Ake

PAPITA pafupi-fupi miyezi iŵili kucokela pamene Aisiraeli anacoka ku Iguputo, ndipo afika pa phili la Sinai. Phili limeneli dzina lake lina ndi Horebe. Pamalo amenewa m’pamene Yehova anakamba ndi Mose kucokela mu citsamba coyaka moto. Aisiraeli akhala pamalo amenewa kwakanthawi.

Pamene Mose akwela mu phili la Sinai limeneli, anthu atsala pansi kuyembekezela. Pamwamba pa phili, Yehova auza Mose kuti afuna kuti Aisiraeli azimvela Iye ndi kuti akhale anthu ake apadela. Mose aseluka mu phili ndi kuuza Aisiraeli zimene Yehova wakamba. Ndipo io akamba kuti adzamvela Yehova, cifukwa afuna kukhala anthu ake.

Pamenepo, Yehova acita cinthu codabwitsa. Acititsa kuti phili liyambe kucotsa utsi pamwamba, ndipo anthu amvela kulila kwa mabingu. Mulungu auza anthu kuti: ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakucotsani ku Iguputo.’ Ndiponso awalamula kuti: ‘Osalambila milungu ina koma ine cabe.’

Mulungu apatsanso Aisiraeli malamulo ena 9. Anthu acita mantha kwambili. Auza Mose kuti: ‘Imwe mukambe ndi ife, cifukwa tiopa kuti ngati Mulungu akamba ndi ife, tidzafa.’

Pambuyo pake, Yehova auza Mose kuti: ‘Kwela mu phili ubwele kwa ine. Ndidzakupatsa miyala iŵili yafulati imene ndalembapo malamulo amene nifuna kuti anthu azitsatila.’ Conco Mose akwelanso mu phili muja. Ndipo akhalako masiku 40, usana ndi usiku.

Mulungu apatsa anthu ake malamulo ambili-mbili. Mose alemba malamulo amenewa. Mulungu apatsanso Mose miyala iŵili yafulati ija. Pamiyala imeneyi, Mulungu mwiniwake walembapo malamulo 10 amene iye anawalankhula kwa anthu onse. Malamulo amenewa amachedwa kuti Malamulo Khumi.

Malamulo Khumi ni ofunika kwambili. Komanso malamulo ena ambili amene Mulungu apatsa Aisiraeli nao ni ofunika. Pamalamulo amenewa, lamulo limodzi limakamba kuti: ‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse.’ Ndipo lina ndi lakuti: ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.’ Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu, anakamba kuti amenewa ndio malamulo aŵili akulu kwambili amene Yehova anapatsa anthu ake Aisiraeli. Kutsogolo tidzaphunzila zambili za Mwana wa Mulungu ndi zimene anaphunzitsa.

Ekisodo 19:1-25; 20:1-21; 24:12-18; 31:18; Deuteronomo 6:4-6; Levitiko 19:18; Mateyu 22:36-40.