Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 43

Yoswa Akhala Mtsogoleli

Yoswa Akhala Mtsogoleli

MOSE afuna kwambili kuloŵa mu dziko la Kanani ndi Aisiraeli. Conco apempha Yehova kuti: ‘Conde ndiloleni ndioloke mtsinje wa Yorodano, kuti ndione dziko labwino.’ Koma Yehova amuuza kuti: ‘Khala cete! Usandiuzenso nkhani iyi!’ Kodi udziŵa cimene Yehova anamuuzila zimenezi?

N’cifukwa ca zimene zinacitika pamene Mose anamenya cimwala ndi ndodo. Ngati ukumbukila, Mose ndi Aroni sanalemekeze Yehova. Iwo sanauze anthu kuti Yehova ndiye anawatulutsila madzi mu cimwala. Cifukwa ca zimene anacita, Yehova anawauza kuti sadzaloŵa mu dziko la Kanani.

Conco patapita miyezi yocepa kucokela pa imfa ya Aroni, Yehova auza Mose kuti: ‘Tenga Yoswa, umuimike pamaso pa Eleazara wansembe ndi pamaso pa anthu. Ndipo uuze anthu onse kuti Yoswa ndiye mtsogoleli wao watsopano.’ Mose acita zimene Yehova wamuuza, monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa.

Ndiyeno Yehova auza Yoswa kuti: ‘Limba mtima, ndipo usacite mantha. Cifukwa udzatsogolela Aisiraeli kuloŵa mu dziko la Kanani limene ndinawalonjeza, ndipo ndidzakhala ndi iwe.’

Pambuyo pake Yehova auza Mose kukwela mu phili la Nebo, m’dziko la Moabu. Ali pamwamba pa phili limenelo, Mose aona mtsinje wa Yorodano ndi dziko lokongola la Kanani. Ndiyeno Yehova amuuza kuti: ‘Dziko lija ndi limene ndinalonjeza ana a Abulahamu, Isaki ndi Yakobo. Ndakuonetsa koma sudzaloŵamo.’

Mose anafela pamwamba pa phili la Nebo. Anafa ali ndi zaka 120. Anali akali ndi wamphamvu, komanso maso ake anali kuona bwino-bwino. Anthu ali ndi cisoni ndipo amulila kwambili. Ngakhale ni conco, iwo ali okondwelabe kuti Yoswa ndiye mtsogoleli wao watsopano.

Numeri 27:12-23; Deuteronomo 3:23-29; 31:1-8, 14-23; 32:45-52; 34:1-12.