Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 107

Anthu Atema Miyala Stefano

Anthu Atema Miyala Stefano

MWAMUNA amene wagwada pacithunzi-thunzi apa ni Stefano. Iye ni wophunzila wokhulupilika wa Yesu. Koma ona zimene zimucitikila! Amunawa amutema miyala ikulu-ikulu. N’cifukwa ciani anthu awa amuzonda kwambili Stefano cakuti acita cinthu coipa ici? Tiye tione.

Mulungu anali kuthandiza Stefano kucita zozizwitsa. Anthu amenewa sakondwela ndi zimene iye acita, conco ayamba kutsutsana naye cifukwa cophunzitsa anthu coonadi. Koma Mulungu apatsa Stefano nzelu zambili, ndipo iye aonetsa kuti zimene anthu awa aphunzitsa n’zabodza. Zimenezi zinawakwiyitsa kwambili. Conco amugwila, ndipo abweletsa anthu kuti amunenele zabodza.

Mkulu wansembe afunsa Stefano kuti: ‘Kodi zimene anena izi n’zoona?’ Stefano awayankha mwa kukamba nkhani yocokela m’Baibo. Potsilizila pake, awauza mmene anthu oipa anazondela aneneli a Yehova m’nthawi zakale. Ndiyeno awauza kuti: ‘Inu ndinu ofanana ndi anthu oipa amene aja. Munapha Yesu mtumiki wa Mulungu, ndipo simumvela malamulo a Mulungu.’

Atsogoleli acipembedzo akalipa kwambili pamene amvela zimenezi! Iwo akukuta mano cifukwa ca ukali. Koma Stefano ayang’ana kumwamba ndi kunena kuti: ‘Onani! Ndiona Yesu kumwamba, waimilila kudzanja lamanja la Mulungu.’ Atamva zimenezi, anthu amenewo atseka makutu ndi manja ao ndi kuthamangila kwa Stefano. Amugwila ndi kumukokela kunja kwa mzinda.

Kumeneko avula malaya ao ovala pamwamba ndi kupatsa wacinyamata Saulo kuti awasungile. Kodi wamuona Saulo pacithunzi-thunzi? Ndiyeno amuna ena anayamba kumutema miyala Stefano. Pamenepo Stefano agwada pansi, monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa, ndi kuyamba kupemphela kwa Mulungu kuti: ‘Yehova, musawalange pa zoipa zimene acita.’ Iye adziŵa kuti ena a io anangopusitsidwa ndi atsogoleli acipembedzo. Pambuyo pake Stefano amwalila.

Munthu wina akakucitila coipa, kodi nawenso umafuna kumucitila coipa kapena ungapemphe Mulungu kuti amulange? Stefano kapena Yesu sanacite zimenezo. Iwo anali okoma mtima ngakhale kwa anthu amene anawacitila zoipa. Ifenso tiyenela kutsatila citsanzo cao.

Machitidwe 6:8-15; 7:1-60.