Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 111

Mnyamata Amene Anagona Tulo

Mnyamata Amene Anagona Tulo

A-AA! Kodi cicitika pacithunzi-thunzi apa n’ciani? Kodi mnyamata amene wagona pansi wazipweteka kwambili? Ona! Mmodzi wa anthu amene acoka m’nyumba ni Paulo! Kodi Timoteyo nayenso wamuona pamenepa? Kodi mnyamata wagwa kucokela pawindo?

Inde, zimenezi ndiye zacitika. Paulo akamba nkhani kwa ophunzila ku Torowa. Iye adziŵa kuti sadzawaonanso kwa nthawi yaitali, cifukwa tsiku lotsatila anali kucoka kumeneko ndi boti. Conco apitiliza kukamba mpaka pakati pausiku.

Koma mnyamata wina dzina lake Utiko wakhala pawindo ndipo wagona tulo. Ndiyeno akugwa kucokela pawindo ya nyumba ya nsanjika zitatu ndi kugwela pansi! Conco ungaone cifukwa cake anthu aoneka ndi nkhawa. Pamene anthu amunyamula mnyamata, cinali coziŵikilatu kuti iye wamwalila!

Pamene Paulo aona kuti mnyamatayo wamwalila, adziponya pamwamba pake ndi kumukumbatila. Ndiyeno akamba kuti: ‘Musadandaule, iye ali bwino-bwino! Ndipo n’zoona kuti ali bwino. Paulo acita cozizwitsa! Iye aukitsa mnyamata wakufayo! Anthu onse akondwela kwambili.

Onse abwelelanso m’cipinda cimene analimo ndi kuyamba kudya cakudya. Paulo apitiliza kukamba mpaka kwaca. Koma n’codziŵikilatu kuti Utiko sanagonenso! Ndiyeno Paulo, Timoteyo ndi ena amene anali kuyenda nao akwela boti. Kodi udziŵa kumene io ayenda?

Paulo wangotsiliza kumene ulendo wake wacitatu wolalikila, ndipo tsopano ali paulendo wopita kwao. Paulendo umenewu, Paulo akhala zaka zitatu mumzinda wa Efeso mokha. Conco ulendo umenewu ni wautali kuposa ulendo wake waciŵili.

Pamene boti yao icoka ku Torowa, iima pang’ono pa Mileto. Popeza mzinda wa Efeso uli pafupi kwambili ndi mzinda wa Mileto, Paulo atumiza uthenga wakuti akulu a mpingo abwele ku Mileto kuti adzakambe nao kotsilizila. Pambuyo pake, pamene nthawi yakuti boti inyamuke ikwana, akuluwo acita cisoni kwambili kuona kuti Paulo ayenda!

Potsilizila pake, boti ibwelelanso ku Kaisareya. Pamene Paulo akhala kumeneku kunyumba ya wophunzila Filipo, mneneli Agabo acenjeza Paulo. Iye akamba kuti Paulo akayenda ku Yerusalemu adzaponyedwa mu ndende. Ndipo zimenezi zicitika zoona. Ndiyeno pambuyo pokhala mu ndende kwa zaka ziŵili mu Kaisareya, Paulo atumizidwa ku Roma kuti akaweluzidwe pamaso pa Wolamulila waciroma Kaisara. Tiye tione zimene zicitika paulendo wao woyenda ku Roma.

Machitidwe macaputa 19 mpaka 26.