Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 108

Paulendo Wa Ku Damasiko

Paulendo Wa Ku Damasiko

KODI uyu amene wagona pansi wamudziŵa? Ni Saulo. Kodi wakumbukila kuti ndiye amene anali kuyang’anila zovala za amuna amene anaponya miyala Stefano? Wakuona kuwala pacithunzi-thunzi apa! Kodi n’ciani cicitika?

Pambuyo pakuti Stefano waphedwa, Saulo atsogolela anthu ofuna-funa otsatila a Yesu kuti awazunze. Iye ayenda nyumba ndi nyumba kukawagwila ndi kuwaponya mu ndende. Ophunzila ambili athaŵila ku mizinda ina, ndipo ali kumeneko ayamba kulalikila “uthenga wabwino.” Koma Saulo ayenda ku mizinda ina kukafuna-funa otsatila a Yesu. Tsopano ali paulendo wopita ku Damasiko. Koma akali m’njila, pacitika cinthu codabwitsa ici:

Mwadzidzidzi kuwala kocokela kumwamba kunangoti ngwee ponse pamene pali Saulo. Iye akugwa pansi monga mmene tionela pacinthunzi-thunzi apa. Ndiyeno mau amveka onena kuti: ‘Saulo, Saulo! N’cifukwa ciani unizunza? Anthu amene ali ndi Saulo aona kuwalako ndipo akumva mauwo, koma samvetsetsa zimene zikambidwa.

Saulo afunsa kuti: ‘Kodi ndinu ndani Mbuyanga?

Mauo akuti: ‘Ndine Yesu, amene iwe uzunza.’ Yesu akamba zimenezi cifukwa cakuti pamene Saulo azunza otsatila ake, Yesu akumva monga iye ndiye azunzidwa.

Tsopano Saulo afunsa kuti: ‘Kodi n’cite ciani Mbuyanga?

Yesu akuti: ‘Nyamuka, ndipo uyende ku Damasiko.’ Kumeneko udzauzidwa cimene uyenela kucita.’ Pamene Saulo anyamuka ndi kutsegula maso, saona ciliconse. Iye akhala wakhungu! Conco amuna amene ali naye amugwila padzanja ndi kumupeleka ku Damasiko.

Ndiyeno Yesu akamba ndi mmodzi wa ophunzila ake ku Damasiko, akuti: ‘Hananiya nyamuka, upite kumseu wochedwa Mseu Woongoka. Ukafika panyumba ya Yudasi, ukafunse za munthu, dzina lake Saulo. Ndamusankha iye kuti akhale mtumiki wanga wapadela.’

Hananiya acita zimene wauzidwa. Pamene akumana ndi Saulo, aika manja pa iye ndi kukamba kuti: ‘Ambuye anituma kwa iwe kuti uyambenso kuona, ndi kutinso udzazidwe ndi mzimu woyela.’ Nthawi imeneyo m’maso mwa Saulo mukugwa tunthu tooneka ngati mamba a nsomba, ndipo ayambanso kuona.

Saulo agwilitsilidwa nchito kwambili polalikila kwa anthu a mitundu yosiyana-siyana. Ndipo achedwa kuti mtumwi Paulo. Tidzaphunzila zambili za iye. Koma coyamba, tiye tione cimene Mulungu atuma Petulo kuti acite.

Machitidwe 8:1-4; 9:1-20; 22:6-16; 26:8-20.