Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 12

Anthu Amanga Cinsanja

Anthu Amanga Cinsanja

PANAPITA zaka zambili. Ana amuna a Nowa anakhala ndi ana ambili. Ana ao anakula ndipo naonso anakhala ndi ana ambili. Tsopano anthu anaculuka kwambili padziko lapansi.

Mmodzi wa anthu amenewa anali mdzukulutuvi wa Nowa, dzina lake anali Nimurodi. Anali munthu woipa amene anali kusaka nyama ndi kupha anthu. Nimurodi anadziika kukhala mfumu kuti azilamulila anthu onse. Mulungu sanamukonde Nimurodi.

Panthawi imeneyi, anthu onse anali kukamba cinenelo cimodzi. Nimurodi anali kufuna kuti anthu onse akhale malo amodzi pofuna kuti aziwalamulila. Kodi udziŵa cimene anacita? Anauza anthu kumanga mzinda wokhala ndi cinsanja cikulu. Ona anthu awa pa cithunzi-thunzi aumba nchelwa.

Yehova sanakondwele naco cimango cimeneci. Sanafune kuti anthu akhale malo amodzi. Anafuna kuti azikhala m’malo osiyana-siyana padziko lonse lapansi. Koma anthu anakamba kuti: ‘Tiyeni timange mzinda ndipo nsanja yake ikafike kumwamba kweni-kweni. Tikacita zimenezi tidzakhala ochuka. Anthu anadzifunila ulemu, m’malo molemekeza Mulungu.

Conco Mulungu anawaletsa kumanga cinsanja cija. Kodi udziŵa kuti anawaletsa bwanji? Mwadzidzidzi anacititsa anthu kuyamba kukamba zinenelo zosiyana-siyana, m’malo mokamba cinenelo cimodzi. Motelo, omanga analeka kumvelana. Ndiye cifukwa cake mzinda wao unachedwa Babele, kapena Babulo, kutanthauza “Msokonezo.”

Anthu anayamba kucoka pa Babele. Anthu amene anali kukamba cinenelo cofanana anapita kukakhala ku malo amodzi, ndipo anthu okamba zinenelo zina anapitanso kumadela ena a dziko lapansi.

Genesis 10:1, 8-10; 11:1-9.