Nkhani 32
Milili 10
YANG’ANA pazithunzi-thunzi izi. Cithunzi-thunzi ciliconse cionetsa mlili umene Yehova anabweletsa mu dziko la Iguputo. Pacithunzi-thunzi coyamba pali Aroni amenya pamtsinje wa Nailo ndi ndodo yake. Pamene anacita zimenezi, madzi a mu mtsinjewo anasanduka magazi. Nsomba zinafa, ndipo mtsinjewo unayamba kununkha moipa.
Cotsatilapo, Yehova anacititsa acule kutuluka mu mtsinje wa Nailo. Acule amenewa anali paliponse, mu mauvuni, mu ziwiya zokanyilamo fulaulo, ndi pa mabedi a anthu. Pamene acule anafa, Aiguputo anawaunjika miyulu miyulu, ndipo dziko lonse linanunkha moipa cifukwa ca acule.
Ndiyeno Aroni anamenya pansi ndi ndodo yake, ndipo fumbi linasanduka nchenche kapena kuti inzi zoluma. Nchenchezo zinali zing’ono-zing’ono koma zoluma. Mlili wanchenche unali wacitatu kucitika mu dziko la Iguputo.
Milili yonse yotsatila inali kugwela Aiguputo okha, osati Aisiraeli. Mlili wacinai unali tudoyo twakumwa magazi tumene tunaloŵa mu nyumba zonse za Aiguputo. Mlili wacisanu unakhudza zinyama. Ng’ombe, nkhosa ndi mbuzi zambili za Aiguputo zinafa.
Ndiyeno, Mose ndi Aroni anatenga phulusa ndi kuliponya m’mwamba. Phulusa limenelo linacititsa anthu ndi zinyama kukhala ndi zilonda zoipa kwambili. Ndipo zilonda zimenezi zinali mlili wa namba 6.
Pambuyo pa zimenezi, Mose ananyamula dzanja lake m’mwamba, ndipo Yehova anatumiza mphezi ndi cimvula ca matalala. Cinali cimvula ca matalala amene sanagwepo mu Iguputo.
Mlili wa namba 8 unali wa dzombe lambili. Kuyambila kale mpaka nthawi imeneyo, sikunagwepo dzombe lambili conco. Linadya zinthu zonse zimene cimvula cija cinasiyako.
Mlili wa namba 9 unali cimdima. Kwa masiku atatu, mu dziko lonse munali cimdima candiweyani, koma kumene Aisiraeli anali kukhala kunali kowala.
Potsilizila pake, Mulungu anauza anthu ake kuti awaze magazi a mwana wa mbuzi, kapena mwana wa nkhosa, pafelemu ya pamwamba pa zitseko zao. Ndiyeno mngelo wa Mulungu anapita mu dziko lonse la Iguputo. Anali kuti akaona magazi pakhomo, sanali kupha munthu aliyense mu nyumbamo. Koma panyumba zonse zimene zinalibe magazi pazitseko, mngelo wa Mulungu anali kupha mwana woyamba wa anthu ndi wa nyama. Umenewu ndio unali mlili wa namba 10
Pambuyo pa mlili wotsilizila umenewu, Farao anauza Aisiraeli kuti apite. Anthu a Mulungu onse anali okonzeka kupita, ndipo usiku umenewo ananyamuka kucoka mu Iguputo.
Ekisodo caputa 7 mpaka 12.