Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 19

Yakobo Ali Ndi Banja Lalikulu

Yakobo Ali Ndi Banja Lalikulu

WALIONA banja lalikulu ili pacithunzi-thunzi! Amenewa ni ana amuna 12 a Yakobo. Iye analinso ndi ana akazi. Kodi ndi maina ati a ana amenewa amene udziŵa? Tiye tidziŵe ena mwa maina amenewa.

Leya anabala Rubeni, Simiyoni, Levi ndi Yuda. Pamene Rakele sanali kubala ana, anakhala wacisoni kwambili. Conco anapeleka Biliha kapolo wake kwa mwamuna wake Yakobo, ndipo Biliha anabala ana amuna aŵili, Dani ndi Nafitali. Ndiyeno Leya nayenso anapeleka Zilipa kapolo wake kwa Yakobo, ndipo Zilipa anabala Gadi ndi Aseri. Koma Leya anabalanso ana amuna ena aŵili, Isakara ndi Zebuloni.

Potsilizila pake, Rakele anabala mwana, ndipo anamupatsa dzina lakuti Yosefe. Panthawi ina tidzaphunzila zambili za Yosefe, cifukwa iye anadzakhala munthu wofunika kwambili. Awa ndiwo ana 11 amene Yakobo anabala pamene anali kukhala kwa Labani, atate a Rakele.

Yakobo analinso ndi ana akazi, koma Baibo imachula dzina la mmodzi cabe. Dzina lake anali Dina.

Nthawi inafika pamene Yakobo anaganiza kuti acoke kwa Labani ndi kubwelela ku Kanani. Conco, anasonkhanitsa banja lake lalikulu pamodzi, ndi nkhosa zake ndi ng’ombe zake zambili. Pamenepo, anayambapo ulendo utali.

Pamene Yakobo ndi banja lake anabwelela ku Kanani ndi kukhalako kanthawi, Rakele anabala mwana wina mwamuna. Mwana ameneyu anabadwa pamene anali paulendo. Rakele anavutika kwambili pobala mwana ameneyu, cakuti potsilizila pake anamwalila. Koma kamwana kanali bwino-bwino. Yakobo anamupatsa dzina lakuti Benjamini.

Tifuna kuti tikumbukile maina a ana 12 a Yakobo cifukwa mtundu wonse wa Isiraeli unacokela mwa ana amenewa. Ndipo maina a mitundu 12 ya Aisiraeli anacokela kwa ana amuna 10 a Yakobo, ndi kwa ana amuna aŵili a Yosefe. Isaki anakhala moyo kwa zaka zambili ana onsewa atabadwa kale, ndipo cinali cokondweletsa kwambili kukhala ndi adzukulu ambili. Koma tiye tione zimene zinacitika kwa mdzukulu wake Dina.

Genesis 29:32-35; 30:1-26; 35:16-19; 37:35.