Nkhani 24
Yosefe Ayesa Abale Ake
YOSEFE afuna kudziŵa ngati abale ake 10 aja akali ouma mtima ndi opanda cifundo. Conco awauza kuti: ‘Inu ndinu akazitape! Ndithu mwabwela kuno kudzafufuza dziko lathu!’
Koma iwo ayankha kuti: ‘Iyai, ife ndife anthu acilungamo. Ndife anthu apaubale umodzi ndipo tinalipo 12. Koma m’bale wathu mmodzi kulibenso, ndipo wamng’ono kwambili watsala ndi atate athu.’
Yosefe saonetsa kuti akhulupilila zimene abale ake akamba. Aponya mu ndende m’bale wake Simiyoni. Koma enawo awalola kuti agule cakudya ndi kubwelela kwao. Koma awauza kuti: ‘Mukadzabwelanso mukabweletse m’bale wanu wamng’ono.’
Pamene abwelela kwao ku Kanani, abale ake afotokozela atate ao, a Yakobo, zonse zimene zinacitika. Yakobo acita cisoni kwambili. Iye alila kuti: ‘Yosefe kulibe ndipo tsopano Simiyoni naye kulibe. Sindidzakulolani kuti mutenge mwana wanga wamng’ono Benjamini.’ Koma pamene cakudya ciyamba kutha, Yakobo awavomeleza kuti Benjamini ayende nao pamodzi ku Iguputo kuti akagule cakudya cina.
Yosefe aona abale ake akubwela. Akondwela kwambili kuona mng’ono wake Benjamini. Koma palibe amene adziŵa kuti munthu waudindoyo ni Yosefe. Ndipo Yosefe acita cinacake kuti awayese abale ake 10 aja.
Iye auza anchito ake kuti adzaze matumba a abale ake onse ndi cakudya. Koma popanda abale ake kudziŵa, awauzanso anchito ake kuti aike cikho cake capadela casiliva mu thumba la Benjamini. Pambuyo pakuti onse apita ndi kuyendako kamtunda pang’ono, Yosefe auza anchito ake kuti awatsatile. Pamene awapeza, awafunsa kuti: ‘N’cifukwa ciani mwaba cikho casiliva ca mbuye wathu?’
Abale ake onse anati: ‘Sitinabe cikho ife. Ndipo mukapeza kuti mmodzi wa ife ali ndi cikho, ameneyo mumuphe.’
Conco anchito aja afuna-funa m’matumba onse, ndipo apeza cikho cimeneci mu thumba la Benjamini, monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa. Anchitowo akamba kuti: ‘Inu nonse yendani, koma Benjamini tibwelela naye.’ Kodi n’ciani cimene abale ake 10 adzacita tsopano?
Onse abwelela pamodzi ndi Benjamini kunyumba kwa Yosefe. Pamenepo Yosefe auza abale ake kuti: ‘Inu nonse mupite kwanu, koma Benjamini adzakhala kuno monga kapolo wanga.’
Ndiyeno Yuda ayankha kuti: ‘Nikabwelela kunyumba popanda mng’ono wanga uyu, atate anga adzamwalila cifukwa amamukonda kwambili. Conde, tengani ine nikhale kuno monga kapolo wanu, koma lolani mng’ono wanga abwelele kunyumba.’
Yosefe aona kuti abale ake anasintha. Iwo salinso ouma mtima ndi opanda cifundo. Tiye tione tsopano zimene Yosefe adzacita.
Genesis 42:9-38; 43:1-34; 44:1-34.